Kodi Kholo Ndani? Nanga Mwana Ndani?
KATSWIRI wa zamaganizo ku California, U.S.A., akundandaula ndi mmene udindo wa makolo waloŵera pansi m’zaka zaposachedwa. “Mu ofesi yanga,” akulemba choncho, “ndaonerera makambitsirano osaŵerengeka pakati pa ana ndi makolo amene amachitika monga ngati kuti ndi pakati pa akuluakulu aŵiri, osati mwana ndi kholo. Makambitsirano ovuta monga a m’malo athu antchito akhala akuchitika okhudza zonse, monga nthaŵi imene ana ayenera kupita kukagona, malipiro ndi ntchito zapakhomo zomwe. Nthaŵi zina kwakhala kovuta kudziŵa kuti kodi kholo ndiponso mwana ndani.”
Baibulo limapereka uphungu woyenera kwa makolo. Limawachenjeza za kuipa kwa kuika malamulo ambiri kwakuti nkufika poŵaŵitsa mtima mwana wawo, mwina kupangitsa mwana kupsinjika maganizo ndi kutaya mtima. (Akolose 3:21) Komabe limachenjezanso makolo kuti asachite kunyanyanso—kumangololera monkitsa, kutayiratu udindo wawo. Miyambo 29:15 imati: “Mwana womlekerera achititsa amake manyazi.” Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Yemwe alera kapolo wake mwaufulu kuyambira ubwana wake, pambuyo pake adzadziyesa mwana wobala [“adzakhala wosayamika,” NW].” (Miyambo 29:21) Ngakhale kuti lembali limanena za kapolo, mfundo yake imagwiranso ntchito ngakhale kwa ana.
Makolo omwe amamana ana awo chitsogozo chofunika ndi chilango pamapeto pake amavutika ndi zotsatira zake—banja losalamulirika. Kuli bwino chotani nanga kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo! Ndithudi, kuchita zimenezo kumafuna khama, koma kukhoza kubweretsa mapindu pamoyo wonse. Baibulo limati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”—Miyambo 22:6.