Linawayambitsa Kulalikira
Mu mzinda wa Khabarovsk, momwe mumakhala anthu pafupifupi 700,000 ku Far East ku Russia, muli mipingo yambiri ya Mboni za Yehova. Akazi ena aŵiri omwe amakhala m’mudzi wa pafupi ndi mzindawo analandira buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Komabe Mbonizo mu Khabarovsk sizinathe kukawachezera kumudzi kwawoko.
Choncho akaziwo anayamba kuphunzira bukulo ndi Baibulo pamodzi m’njira yomwe inali yabwino kwambiri kwa iwo. Atamaliza, anaganiza kuti kunali bwino kuuzako ena zomwe anaphunzira, monga momwe anachitira Akristu oyambirira.—Mateyu 10:7; Machitidwe 20:20.
Pakhomo loyamba limene anafikapo, akaziwo anapeza mwamuna amene anayamba naye phunziro la Baibulo. Patapita kanthaŵi, mkazi wake ndi mwana wake wamkazi anayambanso kukambitsirana nawo Baibulo mokhazikika. Atakumana ndi Mboni zina, onse asanuwo anabatizidwa. Tsopano, akazi aŵiri aja omwe anayamba kuuzako anzawo za uthengawo ndi alaliki a nthaŵi zonse.
Inunso mungayambe kugaŵana ziphunzitso za Baibulo ndi ena ngati mutaŵerenga buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Ngati mungafune kulandira bukuli kapena kuti wina azibwera kudzachita nanu phunziro la Baibulo la panyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena ku keyala yoyenerera ili patsamba 5.