Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g02 8/8 tsamba 32
  • Kutsutsana Pankhani ya Mboni za Yehova Anakuonetsa pa TV

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutsutsana Pankhani ya Mboni za Yehova Anakuonetsa pa TV
  • Galamukani!—2002
Galamukani!—2002
g02 8/8 tsamba 32

Kutsutsana Pankhani ya Mboni za Yehova Anakuonetsa pa TV

M’chaka cha 2000 ndi 2001, anthu ena anaukira Mboni za Yehova m’dziko la Georgia, lomwe kale linali limodzi mwa mayiko a Soviet Union. Pulogalamu inayake yotchuka kwambiri ya pa TV m’dziko la Georgia, anaonetsapo mkangano womwe unalipo pakati pa wandale wina yemwe ankafuna kuti Mboni za Yehova ziletsedwe m’dzikolo, ndi pulofesa wina yemwe khoti linam’sankha kuti afufuze zimene zimalembedwa m’mabuku a Mboni za Yehova.

Potsutsa nkhani zambirimbiri zoipitsa zikhulupiriro za Mboni za Yehova, pulofesayo anati zonena za wandaleyo zinali “zongomva za m’maluŵa basi.” Kenaka iye anatenga buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha n’kulinyamula m’mwamba kuti anthu alione pa TV, n’kunena kuti: “Izi n’zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira.”

Kenaka pulofesayo anayamba kuŵerenga ndime yoyamba ya bukuli yomwe mawu akumapeto kwake amati: “Komabe, kwa anthu ambiri, moyo ukuoneka kukhala wa mavuto aakulu okhaokha. Ngati umenewo ndiwo mkhalidwe wanu, khazikani mtima pansi.”

Buku limeneli limasonyeza mayankho a m’Baibulo a mafunso amene anthu ambiri amafunsa. Mwachitsanzo, mitu yake ina n’njakuti: “Kodi Mulungu Woona Ndani?,” “Kodi N’chifukwa Ninji Timakalamba ndi Kufa?,” ndiponso “Kodi Mulungu Waloleranji Kuvutika?”

Kodi mungafune kuti mulandire buku la masamba 192 limeneli kuti mudzionere nokha mayankho ake? Mungathe kuitanitsa bukuli polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Nditumizireni buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena