“Ndifunika Kuti Ndidziŵe Bwino Nkhaniyi”
CHAKA chatha mkazi wina analemba m’kalata kuti: “Dzulo ndinalandira kabuku kamene ndinapempha kuti anditumizire kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?” Mkaziyu anafotokoza kuti asanalandire kabukuko anali atalandirapo mabuku ena kaŵiri konse ofotokozapo za kabukuka. Iye anati: “Maso ankangokhala ali kunjira podikirira kabuku kameneka chifukwa chakuti nditaŵerenga nkhani zonena za kabukuka, ndinaona kuti ndifunika kuti ndidziŵe bwino nkhaniyi. Nditangolandira kabuku kameneka, sindinachedwe kuyamba kukaŵerenga. Nkhani zonse zimene zili m’kabuku kanu kameneka n’zomveka bwino kwambiri ndipo n’zochokera m’Baibulo.”
Pomaliza mkaziyu anati: “Ndikuona kuti ndibwino kuti ndisachedwe kuyamba kutsatira zimene ndaŵerenga.”
Tikukhulupirira kuti inunso mungapindule mutaŵerenga kabuku kamasamba 32 kameneka kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Kuwonjezera pa phunziro lina losangalatsa limene lili m’kabukuka lakuti “Kodi Yesu Kristu Ndani?” palinso maphunziro ena akuti “Kodi Mulungu Ndani?,” “Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?” ndiponso “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?” Ngati mukufuna kuitanitsa kabuku kanu, lembani zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Nditumizireni kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.