Mayankho Othandiza a Mafunso Amene Mwakhala Mukufunsa!
• Kodi N’chifukwa Ninji Makolo Anga Samandimvetsetsa?
• Kodi N’chifukwa Ninji Amayi ndi Atate Analekana?
• Kodi Ndingapange Motani Mabwenzi Enieni?
• Kodi N’chifukwa Chiyani Ndimachita Tondovi Kwambiri?
• Kodi N’chifukwa Chiyani Achichepere Samaleka Kundivutitsa?
• Bwanji Ponena za Kugonana
Buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza n’losiyana ndi mabuku ena a achinyamata. Linalembedwa atakambitsirana ndi achinyamata ambirimbiri padziko lonse. Ndipo mayankho ake, omwe ngochokera m’Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu, amathandizadi! Mafunso ali pamwambaŵa ndi ena chabe mwa mafunso amene amayankhidwa m’buku la masamba 320 limeneli.
Kuti mulandire buku lanu, mungathe kulemba zofunika m’kabokosi aka n’kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Nditumizireni buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.