Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 8/07 tsamba 32
  • Kodi Chifuno cha Moyo n’Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chifuno cha Moyo n’Chiyani?
  • Galamukani!—2007
Galamukani!—2007
g 8/07 tsamba 32

Kodi Chifuno cha Moyo n’Chiyani?

◼ Kwa zaka zambiri anthu anzeru, akatswiri a zaumulungu, ndi anthu wamba ayesetsa mwakhama kufufuza yankho la funso lomwe lili pamwambali koma sanalipeze. Choncho, ambiri amaganiza kuti funso limeneli lilibe yankho. Koma yankho lake lilipo. Ngakhale kuti yankholo ndi lozama, si lovuta kumva.

Yankho lake likupezeka m’Baibulo. Kuti munthu akhale ndi moyo wabwino ndi wosangalala, ayenera kudziwa chifukwa chake Mulungu walola mavuto ambiri ndi kupanda chilungamo kuchitika, kenako ayenera kukhala pa ubale wabwino ndi iye. Koma kodi munthu angachite bwanji zimenezi? Kabuku kamasamba 32 kakuti Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani? kathandiza anthu ambiri kuchita zimenezi.

Ngati mukufuna kuitanitsa kabukuka, lembani zofunika m’mizere ili panoyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani?

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena