Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/07 tsamba 32
  • Mmene Mungakhalire Bwenzi la Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungakhalire Bwenzi la Mulungu
  • Galamukani!—2007
Galamukani!—2007
g 11/07 tsamba 32

Mmene Mungakhalire Bwenzi la Mulungu

◼ Zimenezo n’zimene kabuku ka masamba 32 kakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! kamatiphunzitsa. Mitu ina yosangalatsa m’kabukuka ndi monga yakuti “Mulungu Akukuitanani Kuti Mukhale Bwenzi Lake” ndi “Mulungu Ndiye Bwenzi Labwino Koposa, Limene Mungakhale Nalo.” Kabukuka anakalemba m’njira yoti kathandize munthu amene akuwerengayo kudziwa mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo.

M’mutu wakuti “Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso,” kabukuka kamafotokoza momveka bwino cholinga cha Mulungu cha dziko lathu lapansi. Komabe, kuti tidzasangalale ndi Paradaiso amene Baibulo likulonjeza, tiyenera kudziwa kuti kodi Mulungu amafuna tizimutumikira bwanji. Mitu monga yakuti “Mmene Mungapezere Chipembedzo Choona” ndi “Kanani Chipembedzo Chonyenga!” idzakuthandizani kuti mukhale bwenzi la Mulungu ndiponso kuti Mulunguyo azisangalala nanu. Tikukhulupirira kuti mupindula kwambiri mukawerenga kabuku kameneka.

Ngati mukufuna kuitanitsa kabukuka, lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!

□ Nditumizireni munthu kuti aziphunzira nane Baibulo panyumba kwaulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena