Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 3/10 tsamba 32
  • Yesu Anapereka Moyo Wake Kuti Awombole Anthu Ambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anapereka Moyo Wake Kuti Awombole Anthu Ambiri
  • Galamukani!—2010
Galamukani!—2010
g 3/10 tsamba 32

Yesu Anapereka Moyo Wake Kuti Awombole Anthu Ambiri

Yesu Khristu anauza otsatira ake kuti iye “sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) Iye anapereka moyo wake mofunitsitsa kuti apulumutse anthu.

Kodi imfa ya Yesu inatiwombola bwanji? Kodi n’chifukwa chiyani tinafunikira nsembe? Kodi Yesu anafera ndani? Ndipo kodi imfa yake ndi yofunika bwanji kwa inuyo?

Ife Mboni za Yehova tikukuitanani kuti mudzapezeke nawo pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu kuti mudzapeze mayankho a mafunso amenewa. Chaka chino mwambo umenewu udzachitika Lachiwiri, pa March 30, dzuwa litalowa. Mafunso amene tatchula pamwambawa adzayankhidwa pa tsiku limeneli pogwiritsa ntchito Baibulo.

Tikukupemphani kuti mudzapite ku Nyumba ya Ufumu ya pafupi ndi kwanuko. Kuti mudziwe nthawi ndi malo enieni kumene kudzachitikire mwambowu, funsani Mboni za Yehova za m’dera lanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena