Kodi N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudziwa Uthenga wa M’Baibulo?
● Baibulo ndi buku limene lafalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse m’mbiri yonse ya anthu, ndipo anthu ambiri amalikonda. Anthu amalumbira m’makhoti atagwira Baibulo ndiponso akuluakulu a boma akamaikidwa pa udindo amalumbiritsidwa ataika dzanja lawo pa Baibulo. Munthu akaphunzira Baibulo ndiye kuti waphunzira zinthu zofunika kwambiri kuposa zonse.
Anthu ambiri angavomereze kuti padzikoli bwenzi zinthu zili bwino kwambiri anthu ambiri akanati aziwerenga Baibulo n’kumatsatira zimene limanena. Kabuku kamasamba 32 kakuti Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? kangakuthandizeni kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Kabukuka kali ndi zithunzi zokongola kwambiri. Zigawo ziwiri zoyambirira za kabukuka zimafotokoza zimene Mlengi anachita kuti anthu akhale m’paradaiso komanso zimene zinachitika kuti anthuwo asakhalenso m’paradaiso. Zigawo zotsatira zikufotokoza mbiri ya mtundu umene Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu anadzabadwiramo. Ufumu umenewu ndi umene udzabwezeretse Paradaiso pa dziko lapansi.
Zigawo zotsatira zikufotokoza za moyo, utumiki, zozizwitsa, imfa ndi kuuka kwa Yesu Khristu, yemwe ndi Wolamulira wosankhidwa ndi Mulungu. Zigawo zinayi zotsatira zikufotokoza mwachidule koma mochititsa chidwi kwambiri za otsatira a Yesu oyambirira. Zikufotokoza za utumiki wawo, mmene iwo anakhalirabe okhulupirika pozunzidwa ndiponso za mabuku a m’Baibulo amene iwo anauziridwa kulemba. Mudzasangalala kwambiri powerenga chigawo chakuti “Dziko Lapansi Lidzakhalanso Paradaiso,” komanso tsamba lomaliza la chigawo chimenechi lokhala ndi zithunzi zokongola, la mutu wakuti “Onani Uthenga wa M’Baibulo Mwachidule.”
Ngati mukufuna kabukuka, lembani adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yoyenera pa maadiresi omwe ali patsamba 5 m’magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire kabukuka.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.