Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/13 tsamba 12-13
  • Dziko la Indonesia

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Indonesia
  • Galamukani!—2013
Galamukani!—2013
g 4/13 tsamba 12-13

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Indonesia

DZIKO la Indonesia linapangidwa ndi zilumba zokwana 17,000. Anthu ake amadziwika kuti ndi okonda kulandira alendo, ochezeka, aulemu, komanso ofatsa.

Anthu a ku Indonesia amakonda kudya mpunga ndi ndiwo zothira zokometsera komanso amakonda zipatso. M’madera ena, anthu amadya atakhala pamphasa ndipo amadya ndi manja. Anthu ambiri a ku Indonesia amanena kuti chakudya chimakoma kwambiri akamadya ndi manja komanso atakhala pansi.

Anthu a ku Indonesia amakonda zojambulajambula, kuvina komanso kuimba. Chipangizo chotchuka kwambiri ndi anklong, chomwe amachipanga pogwiritsa ntchito nsungwi zokhala ndi mphako. Nsungwizo amazimangirira kuchithabwa ndipo amazichuna kuti ziziimba mosiyanasiyana akamazigwedeza. Akafuna kuimba nyimbo, nthawi zambiri pamakhala anthu angapo ndipo aliyense amakhala ndi chipangizo chake chomwe amachigwedeza mogwirizana ndi anzakewo kuti nyimboyo imveke bwino.

M’zaka za m’ma 1400 C.E., zipembedzo zotchuka kwambiri ku Indonesia zinali Chihindu ndi Chibuda. Koma pofika m’ma 1500, Chisilamu chinali chitafalikira m’madera ambiri. Kenako pasanapite nthawi, azungu anabwera kudzafunafuna zokometsera ndiwo ndipo anayambitsa Chikhristu.

A Mboni za Yehova, omwe amadziwika ndi ntchito yophunzitsa Baibulo padziko lonse, akhala akugwira ntchito imeneyi ku Indonesia kuyambira mu 1931. Panopa m’dzikoli muli Mboni za Yehova zokwana 22,000, ndipo akuyesetsa kulalikira uthenga wabwino ngakhale kwa anthu ogontha. Mwachitsanzo, chaka chatha anthu oposa 500, anapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu womwe unachitika m’chinenero cha manja.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI FUNSO ILI?

Pa zinthu zili m’munsizi, kodi ndi zinthu ziti zomwe mukuganiza kuti zimapezeka kuti Indonesia?

  1. Mitundu yokwana 20,000 ya zomera

  2. Mitundu yosiyanasiyana ya nyama zazikulu padziko lonse zomwe zimayamwitsa

  3. Mtundu wa maluwa aakulu kwambiri padziko lonse

  4. Mtundu wa maluwa aatali kwambiri padziko lonse

Yankho: Mayankho onse ndi olondola. Duwa lalikulu kwambiri padziko lonse limakula kufika masentimita 91 likatambasula ndipo duwa lalitali kwambiri limatalika kufika mamita atatu.

DZIWANI IZI

  • Kuli anthu okwana: 237,600,000

  • Likulu lake: Jakarta

  • Nyengo: N’kotentha koma nthawi zina kumagwa mvula

  • Zimene amagulitsa kumayiko ena: Mafuta, labala, malasha

  • Zilankhulo: Chiindonesia cha Chibahasa komanso zinenero zina zambiri

  • Chipembedzo: Ambiri ndi Asilamu (Anthu 88 pa 100 alionse ndi Asilamu)

Magazini ya Galamukani! imafalitsidwa m’zinenero 98, kuphatikizapo Chiindonesia (chomwe chimatchedwanso Chiindonesia cha Chibahasa)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena