Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 6/13 tsamba 8-10
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amakonda Kugula Katundu Wambirimbiri?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amakonda Kugula Katundu Wambirimbiri?
  • Galamukani!—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Luso la Kukopa
    Galamukani!—1998
  • N’chifukwa Chiyani Sindikuyenera Kutsanzira Khalidwe la Anthu Omwe Amaonetsedwa M’mafilimu, pa TV ndi M’magazini?—Gawo 1
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Mungatani Kuti Musamangogula Zinthu Mwachisawawa?
    Galamukani!—2013
  • N’chifukwa Chiyani Sindikuyenera Kutsanzira Khalidwe la Anthu Omwe Amaonetsedwa M’mafilimu, pa TV ndi M’magazini?​—Gawo 2: Ya Anyamata
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Galamukani!—2013
g 6/13 tsamba 8-10

NKHANI YA PACHIKUTO: KODI N’KULAKWA KUGULA KATUNDU WAMBIRIMBIRI?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amakonda Kugula Katundu Wambirimbiri?

Lipoti limene linatulutsidwa mu 2012, lonena za kafukufuku amene anachitika padziko lonse, linasonyeza kuti hafu ya anthu amene anafunsidwa anavomereza kuti anagulapo zinthu zimene sizinali zofunika kwenikweni. Lipotilo linasonyezanso kuti anthu awiri pa atatu alionse amaona kuti anthu akumakonda kugula katundu wambiri. Zimenezi n’zoona chifukwa anthu ambiri akumakhala ndi ngongole zomwe akulephera kuzibweza. Akatswiri amene anachita kafukufukuyo ananena kuti kugula zinthu zambiri kumapangitsa munthu kukhala ndi nkhawa komanso amakhala wosasangalala. Nanga n’chiyani chimapangitsa kuti anthu azigula katundu wambirimbiri?

ANTHU amalonda amatsatsa makasitomala zinthu zosiyanasiyana. Koma kodi cholinga chawo chimakhala chiyani kwenikweni? Amafuna kuti anthu aziona zinthu zosafunika kwenikweni ngati zofunika kwambiri pamoyo wawo. Otsatsa malonda amadziwanso kuti nthawi zambiri anthu amagula katundu ngati akopeka naye. Ndiye amatsatsa malonda awo kapena amaika katundu wawo m’shopu mokopa makasitomala.

Buku lina linanena kuti: “Anthu ambiri akafuna kugula chinthu, amadziona m’maganizo mwawo akufunafuna chinthucho m’shopu, atachipeza kenako chitakhala chawo.” (Why People Buy Things They Don’t Need) Akatswiri ena amanena kuti anthu ena amasangalala kwambiri akamagula zinthu moti amangogula zinthu mosaganizira. Katswiri wina woona za malonda, dzina lake Jim Pooler, ananena kuti: “Wogulitsa malonda akaona kuti kasitomala wakomedwa amatengerapo mwayi n’kumunyengerera kuti agule katundu wambiri.”

Kodi mungatani kuti ogulitsa malonda asamakunyengerereni kuti mugule katundu amene simunakonzekere kugula? Musamangokomedwa ndi kugula katunduyo ndipo muziganizira ngati zimene amalondawo akunena zili zoona.

AMALONDA AMAFUNA TIZIGANIZA KUTI: Tikagula katundu wambiri tikhala ndi moyo wosangalala

Aliyense amafuna kukhala ndi moyo wosangalala. Amalonda amafuna tiziganiza kuti tikagula katundu wawo ndiye kuti tikhala ndi thanzi labwino, tikhala otetezeka, opanda nkhawa komanso tizikondana kwambiri ndi achibale komanso anzathu.

ZOONA ZAKE:

Nthawi zambiri munthu akakhala ndi katundu wochuluka sasangalala. Tikutero chifukwa chakuti pamafunika nthawi komanso ndalama zambiri zosamalirira katunduyo. Komanso munthuyo amakhala ndi nkhawa chifukwa cha ngongole ndipo sakhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi achibale komanso anzake.

Mfundo yofunika kuiganizira: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.

AMALONDA AMAFUNA TIZIGANIZA KUTI: Tikagula katundu wambiri anzathu azitisirira

Si onse amene amavomera kuti amagula katundu wambiri n’cholinga choti anzawo aziwasirira. Koma Jim Pooler ananena kuti: “Nthawi zambiri anthu akamagula zinthu amakhala ndi cholinga choti anzawo, aneba awo, anzawo akuntchito komanso achibale awo aziwasirira.” N’chifukwa chake amalonda amagwiritsa ntchito anthu otchuka komanso olemera potsatsa malonda awo. Iwo amafuna anthu aziganiza kuti: “Ndikagula katunduyu ndifanana ndi munthu wolemerayo.”

ZOONA ZAKE:

Munthu akamachita zinthu podziyerekezera ndi anthu ena sakhutira ndi zimene alinazo. Amati akapeza zimene amafuna amayambanso kufuna zinthu zina zatsopano.

Mfundo yofunika kuiganizira: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva.”—Mlaliki 5:10.

AMALONDA AMAFUNA TIZIGANIZA KUTI: Tikagula katundu wambiri tikhala otchuka

Buku lina linanena kuti: “Njira yabwino yodziwitsira anthu kuti siiwe munthu wamba (kapena sukufuna kukhala munthu wamba) ndi kugula zinthu zambiri komanso zapamwamba.” (Shiny Objects) Amalonda amadziwa zimenezi choncho iwo amayesetsa kupanga katundu wapamwamba woti anthu akagula azidziona kuti ndi anthu apamwamba.

Kodi inuyo mumadziona kuti ndinu munthu wotani? Nanga mumafuna kuti anthu azikuonani kuti ndinu munthu wotani? Kodi mumafuna kuti anthu azikuonani kuti ndinu munthu wokonda mafashoni? Kapena mumafuna azikuonani kuti ndinu wotchuka ngati osewera mpira? Amalonda amafuna muziganiza kuti mukagula katundu wapamwamba kwambiri anthu azikuonani kuti ndinu munthu wapamwamba.

ZOONA ZAKE:

Ngakhale katundu atakhala wapamwamba bwanji, sangathandize munthu kukhala ndi makhalidwe abwino monga kuona mtima komanso kukhulupirika.

Mfundo yofunika kuiganizira: “Kudzikongoletsa kwanu kusakhale . . . kuvala zodzikongoletsera zagolide, kapena kuvala malaya ovala pamwamba. Koma kukhale kwa munthu wobisika wamumtima.”—1 Petulo 3:3, 4.

Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Katundu

Taona kuti zimene amalonda amafuna kuti tiziganiza sizikhala zoona. Koma pali buku lina limene lili ndi malangizo amene angatithandize kuti tikhale ndi moyo wosangalala. Mfundo zomwe zili ndi kamutu kakuti “Mfundo yofunika kuiganizira,” n’zochokera m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Baibulo silimaletsa kugula kapena kukhala ndi katundu wambiri. Koma limatiphunzitsa kuti munthu amakhala wosangalala ngati ali ndi moyo “wosakonda ndalama.”—Aheberi 13:5.

Njira Zina Zotsatsira Malonda

Masiku ano makampani akumatsatsa malonda pa TV, m’nyuzipepala komanso pa Intaneti. Kuwonjezera pa zimene tatchulazi, mayiko ena akumagwiritsa ntchito njira zotsatirazi:

KUTSATSA MALONDA MWACHINSINSI: Amalonda amaonetsa katundu wawo m’mapulogalamu a pa TV, mavidiyo komanso m’masewera a pa kompyuta.

KUCHEMERERA: Makampani ena amalipira anthu kuti aziuza anzawo komanso kuti azichemerera katundu amene kampaniyo imagulitsa koma asamadzionetsere kuti atumidwa ndi kampaniyo.

KUIKA NDEMANGA PA INTANETI: Makampani ena amalipira anthu kuti azikalemba pa Intaneti ndemanga zabwino zokhudza katundu amene iwo amagulitsa. Makampaniwa amapatsa anthuwa katunduyo kapena zinthu zina n’cholinga choti azilimbikira kuwatsatsira malondawo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena