Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 6/13 tsamba 12-13
  • Panama

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Panama
  • Galamukani!—2013
Galamukani!—2013
g 6/13 tsamba 12-13

ANTHU NDI MAYIKO

Panama

KU PANAMA n’kotchuka kwambiri chifukwa cha ngalande yaikulu yomwe imalumikizitsa nyanja ya Atlantic ndi ya Pacific. Komanso anthu a ku North ndi South America amadutsa ku Panama akafuna kuyenderana. M’dzikoli muli anthu a mitundu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Ambiri mwa anthu akumeneku makolo awo anachokera ku Ulaya.

Mu 1501, anthu ofufuza malo ochokera ku Spain anayamba kufika ku Panama ndipo anapeza mitundu yosiyanasiyana ya anthu, yomwe ina imapezekabe mpaka pano. Umodzi mwa mitundu imeneyi ndi mtundu wa anthu otchedwa Guna (womwe poyamba unkadziwika kuti Kuna). Anthu ambiri a mtundu umenewu amapezeka pa zilumba za San Blas zomwe zili m’mphepete mwa nyanja ya Pacific kumalire a dziko la Panama ndi Colombia. Iwo amasaka nyama, kuwedza nsomba komanso kulima.

Anthu a mtundu wa Guna amati mwamuna akakwatira amakakhala kuchikamwini. Koma akabereka mwana wamkazi amasamuka kuchikamwiniko n’kukayamba kukhala kwaokha.

Ku Panama kuli mipingo ya Mboni za Yehova pafupifupi 300. Mipingo yambiri ndi ya Chisipanishi koma ina ndi ya Chitchainizi, Chingelezi, Chigujarati, Chiguna, Chikiliyo cha ku Haiti, Chingabere ndi Chinenero chamanja cha ku Panama.

DZIWANI IZI

  • Kuli anthu okwana: 3,629,000

  • Likulu: Panama City

  • Chilankhulo: Chisipanishi

  • Boma: Demokalase

  • Nyengo: N’kotentha koma nthawi zina kumagwa mvula

  • Dera lake: Kuli mapiri a mitengo, udzu komanso nkhalango zambiri. Kulinso zilumba zoposa 1,600

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena