Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 3/14 tsamba 10-11
  • Dziko la El Salvador

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la El Salvador
  • Galamukani!—2014
Galamukani!—2014
g 3/14 tsamba 10-11
Dziko la El Salvador

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la El Salvador

Mapu a dziko la El Salvador

ANTHU a ku Spain anafika m’dziko limene masiku ano limatchedwa El Salvador, pafupifupi zaka 500 zapitazo. Pa nthawiyo mtundu wa anthu amene anali ambiri m’dzikoli unkatchula dziko lawoli kuti Cuscatlán, kutanthauza, “Dziko la Zinthu Zamtengo Wapatali.” Masiku ano anthu amene amapezeka ku El Salvador ndi mbadwa za mitundu ya anthu a m’dzikoli komanso anthu amene anachokera ku Ulaya.

Anthu a ku El Salvador ndi olimbikira ntchito, ansangala komanso aulemu. Asanayambe kucheza kapena kukambirana ndi munthu amayamba apatsana kaye moni. Ukakhala m’mawa amanena kuti “Buenos días” (kutanthauza, mwadzuka bwanji) ndipo akakhala masana amati “Buenas tardes” (kutanthauza, mwaswera bwanji). Ndipotu anthu a m’madera akumidzi amaona kuti kungomudutsa munthu popanda kupereka moni, ndi mwano.

Mayi akutchola khofi

Dziko la El Salvador limadziwika bwino chifukwa cha ulimi wa khofi

Anthu a ku El Salvador amakonda chakudya chotchedwa pupusa. Chakudya chimenechi amachipanga pogwiritsa ntchito ufa wa chimanga kapena wa mpunga ndipo amaphatikiza ndi tchizi, nyemba, nyama ya nkhumba kapena zinthu zina. Nthawi zambiri pakudya chakudyachi amadyera limodzi ndi msuzi wa tomato kapena wopangidwa pophatikiza kabichi, kaloti, anyezi ndi viniga. Ngakhale kuti anthu ena amadya chakudyachi pogwiritsa ntchito mpeni ndi foloko, anthu ambiri amakonda kudya ndi manja.

Chakudya chotchedwa Pupusas

Chakudya chimene anthu a ku El Salvador amakonda kudya chotchedwa Pupusa

Mathithi a Los Tercios

Mathithi otchedwa Los Tercios ku Suchitoto

KODI MUKUDZIWA? M’dziko la El Salvador mumaphulika mapiri. M’dzikoli muli mapiri 20 amene amakonda kuphulika, ndipo ena mwa mapiri amenewa ndi oti angathe kuphulika nthawi ina iliyonse. Mathithi a Los Tercios ndi aatali kwambiri ndipo anabwera chifukwa cha mapiri amene anaphulika.

M’dziko la El Salvador muli a Mboni za Yehova oposa 38,000 ndipo a Mboniwa ali m’mipingo pafupifupi 700. Iwo amaphunzitsa Baibulo anthu pafupifupi 43,000 ndipo amaphunzira nawo m’Chisipanishi, Chingelezi komanso chinenero chamanja cha ku El Salvador.

DZIWANI IZI

  • Kuli anthu okwana: 6,267,000

  • Likulu: San Salvador

  • Chilankhulo: Chisipanishi

  • Nyengo: N’kotentha kwambiri m’mphepete mwa nyanja komanso m’zigwa

  • Dera lake: Dzikoli ndi lamapiri

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Zoona kapena zabodza.

  1. Dziko la El Salvador ndi laling’ono kwambiri pa mayiko onse a ku Central America.

  2. Dziko la El Salvador ndi limene lili ndi anthu ambiri ku Central America.

  3. Zakudya zambiri za anthu a ku El Salvador amaikamo tsabola wambiri.

  4. Dziko la El Salvador limadziwika ndi ulimi wa khofi.

Mayankho: A, B, ndi D, zoona. Yankho la C ndi, zabodza. Anthu ambiri okacheza ku El Salvador amaona kuti zakudya za m’dzikoli samaikamo tsabola wambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena