Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/15 tsamba 10-11
  • Dziko la Costa Rica

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Costa Rica
  • Galamukani!—2015
Galamukani!—2015
g 1/15 tsamba 10-11
Chithunzi chosonyeza mphepete mwa nyanja ku Costa Rica

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Costa Rica

Mapu osonyeza dziko la Costa Rica

ZAKA 500 zapitazo, anthu ochokera ku Spain anafika m’dziko la Costa Rica. Anthuwa ndi amene anapatsa dzikoli dzina lakuti Costa Rica poganiza kuti m’derali apezamo golide wambiri. Koma izi si zimene zinachitika. Masiku ano dziko la Costa Rica silimadziwika kuti lili ndi miyala ya mtengo wapatali. Koma limadziwika kuti lili ndi mitengo komanso nyama zambiri zachilengedwe.

Anthu a ku Costa Rica amatchulidwa kuti Atiko. Dzinali linabwera chifukwa choti anthuwa amawonjezera mawu otanthauza ‘chaching’ono’ kapena ‘chochepa’ kumapeto kwa mawu a chinenero chawo. Amakondanso kunena mawu akuti “¡pura vida!” kutanthauza “moyo wabwino.” Amanena mawuwa posonyeza kuyamikira, kuvomereza, podutsana ndi anthu kapena potsanzika.

Chule wa maso ofiira

Nkhalango za ku Costa Rica zili ndi mitengo komanso nyama zosiyanasiyana. Zina mwa nyamazi ndi achule a maso ofiira

Anthu a ku Costa Rica amakonda kudya chakudya chotchedwa gallo pinto. Pokonza chakudyachi, amaphika mpunga ndi nyemba kenako n’kuzisakaniza ndipo amathiramonso zokometsera zina ndi zina. Chakudyachi akhoza kuchidya m’mawa, masana kapena madzulo. Amakondanso kumwa khofi wotchedwa café chorreado. Akamapanga khofiyu, amamusefa pogwiritsa ntchito kansalu komwe amakaika pakathabwa ndipo khofiyo amagwera m’kapu.

M’dziko la Costa Rica muli mipingo ya Mboni za Yehova pafupifupi 450. Misonkhano yawo imachitika m’chinenero chamanja cha komweko, m’Chibiribiri, m’Chikabeka komanso mu zinenero zina 7. Chibiribiri ndi Chikabeka ndi zinenero za nzika za m’dzikoli.

KODI MUKUDZIWA? Ku Costa Rica anapezako miyala yambirimbiri yozungulira ndipo ina ya miyalayi ndi yaikulu kwambiri. Ena amaganiza kuti miyalayi yakhalapo kwa zaka zoposa 1,400. Anthu sadziwa kuti miyalayi ankaigwiritsa ntchito yanji kalelo.

Miyala yozungulira ya ku Costa Rica

Miyala yozungulira

MFUNDO ZACHIDULE

  • Chiwerengero cha anthu: 4,878,000

  • Likulu: San José

  • Chinenero chachikulu: Chisipanishi

  • Dera lake: M’mphepete mwa nyanja muli zigwa ndipo chapakati pali mapiri

  • Boma: Demokalase

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi ndi ziganizo ziti zimene zikunena zoona zokhudza dziko la Costa Rica?

  1. Anthu ambiri a m’dzikoli ndi ophunzira kwambiri

  2. Lili ndi gulu lamphamvu la asilikali

  3. Lili ndi chilumba chomwe magulu a anthu ofufuza malo oposa 500 anafikako n’cholinga chopeza miyala ya mtengo wapatali

Mayankho: A ndi C. Chiganizo cha C chikunena za chilumba cha Cocos chomwe chili pamtunda wa makilomita pafupifupi 564, kumadzulo kwa dzikoli.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena