Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g16 No. 5 tsamba 10-11
  • Chinthu Chodabwitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chinthu Chodabwitsa
  • Galamukani!—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Maelementi Anakhalako Mwamwayi?
    Galamukani!—2000
  • Kayendedwe ka Mpweya ndi Zinthu Zina
    Galamukani!—2009
  • Kodi Ndani Ali ndi Pensulo?
    Galamukani!—2007
  • Dziko Lathu Losakazidwa Kusakazako Kumakantha Madera Ambiri
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—2016
g16 No. 5 tsamba 10-11

Chinthu Chodabwitsa

Kaboni

Chinthu chodabwitsachi ndi kaboni yemwe amapezeka m’zinthu zamoyo komanso zinthu zina zambiri za m’chilengedwe. Buku lina linati: “Kaboni ndi chinthu chofunika kwambiri kuti moyo upangidwe.” (Nature’s Building Blocks) Kaboni ndi wodabwitsa chifukwa amatha kulumikizana yekhayekha komanso ndi zinthu zina zosiyanasiyana. Nthawi zonse asayansi amatulukira zinthu zatsopano zimene zinapangidwa chifukwa choti kaboni analumikizana ndi zinthu zina komanso amapeza njira zimene angalumikizire kaboni ndi zinthu zina zatsopano.

Monga mmene tingaonere m’zithunzizi, kaboni amatha kulumikizana yekhayekha n’kumaoneka mosiyanasiyana. Mwachitsanzo angaoneke ngati matcheni, maring’i komanso machubu. Kunena zoona kaboni ndi chinthu chodabwitsadi.

DAYAMONDI

Dayamondi

Kaboni amatha kulumikizana ndi kaboni wina n’kumaoneka mmene akuonekera m’chithunzichi. Akalumikizana chonchi amalimba kwambiri ndipo amakhala dayamondi, womwe ndi mwala wamtengo wapatali kwambiri.

GIRAFAITI (GRAPHITE)

Pensulo yamakala

Kaboni amathanso kulumikizana n’kumaoneka mmene akuonekera m’chithunzichi. Akaoneka chonchi amatha kuunjikika ngati mapepala ndipo mbali imodzi ingachoke pamwamba pa zinzake ngati mmene pepala lingachotsedwere pa mapepala ena. Chifukwa cha zimenezi anthu amaika girafaiti pakati pa zinthu zomwe sakufuna kuti zizikhulana kapena kumatirirana. Girafaiti amamugwiritsanso ntchito popanga mapensulo.a

GIRAFINI (GRAPHENE)

Mzere wolemba ndi pensulo

Girafini amapangidwanso kaboni akalumikizana yekhayekha ndipo amaoneka ngati neti, mofanana ndi mmene zikuonekera m’chithunzichi. Girafini ndi wamphamvu kwambiri moti sangaduke msanga poyerekezera ndi chitsulo. Pensulo yamakala imathanso kukhala ndi Girafini koma wochepa kwambiri.

FULARINI (FULLERENES)

Fularini

Fularini amapangidwa kaboni akaphatikizana ndi kaboni wina n’kupanga timipira kapena timachubu ting’onoting’ono kwambiri. Fularini ndi wamng’ono kwambiri moti pomuyeza amagwiritsa ntchito muyezo wopangidwa ndi kagawo kamodzi ka mita imene yagawidwa m’magawo 1 biliyoni.

ZINTHU ZAMOYO

Zinthu zamoyo zokhala ndi kaboni

Kaboni amapezeka mu maselo a zomera, a nyama ndiponso anthu. Zili choncho chifukwa amapezeka m’zinthu monga mafuta komanso michere ya m’thupi.

“Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera . . . m’zinthu zimene anapanga.”—Aroma 1:20.

a Onani nkhani yakuti, “Kodi Ndani Ali ndi Pensulo?” mu Galamukani! ya July 2007.

Nyenyezi

Kaboni Amapangidwa M’nyenyezi

Kaboni amapangidwa mbali zitatu za mpweya winawake zikaphatikizana ndipo asayansi amaganiza kuti zimenezi zimachitika mkati mwa nyenyezi zikuluzikulu zinazake. Koma kuti izi zichitike, pali zinthu zina zimene zimayenera kuchitika ndendende m’njira inayake. Katswiri wina wa sayansi dzina lake Paul Davies ananena kuti “zinthu zikangochitika mosiyana pang’ono ndi njirayo,” mbalizo sizingaphatikizane ndipo “zamoyo, anthu komanso zinthu zonse za m’chilengedwe sizingakhalepo.” Koma kodi n’chiyani chimachititsa kuti zinthu zizichitika ndendende mmene ziyenera kuchitikira kuti kaboni apangidwe? Anthu ena amanena kuti zimangochitika zokha. Pomwe ena amaona kuti ndi umboni woti kuli Mlengi wanzeru. Nanga inuyo mukuganiza bwanji?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena