Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g17 No. 6 tsamba 10-11
  • Dziko la New Zealand

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la New Zealand
  • Galamukani!—2017
Galamukani!—2017
g17 No. 6 tsamba 10-11
Milford Sound, ku New Zealand

Milford Sound

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la New Zealand

Mapu a padziko lonse osonyeza dziko la New Zealand

PAFUPIFUPI zaka 800 zapitazo, anthu a mtundu wa Maori anasamuka ku Polynesia n’kuyenda mtunda wautali kwambiri panyanja yayikulu n’kukakhazikika ku New Zealand. Ku Polynesia n’kotentha kwambiri kusiyana ndi ku New Zealand. Ku New Zealand kuli mapiri ambiri, madzi oundana, akasupe amadzi otentha komanso kumagwa sinowo kapena kuti chipale chofewa. Patatha zaka 500, anthu enanso ochokera ku Europe komwe ndi kutali kwambiri, anabwera kudzakhazikika m’dzikoli. Chikhalidwe cha anthu a ku New Zealand panopo, n’chosakanikirana ndi cha anthu a ku Britain, Germany komanso Polynesia. Anthu pafupifupi 90 pa 100 aliwonse m’dzikoli, amakhala m’tauni. Mzinda wa Wellington womwe ndi likulu la dzikoli, umadziwika kuti ndi likulu la kum’mwera kwenikweni kwa dziko lapansi.

Ziphalaphala zowira zochokera pansi panthaka ku North Island m’dziko la New Zealand

Ziphalaphala zowira zochokera pansi panthaka ku North Island

Dziko la New Zealand lili ndi malo ambiri ochititsa chidwi. Choncho ngakhale kuti lili kutali kwambiri, alendo pafupifupi 3 miliyoni amalowa m’dzikoli chaka chilichonse kudzaona malowa.

Mitengo ya Silver fern

Mtengo wa silver fern umatalika kuposa mamita 10

Mbalame ya takahe. Mbalameyi siuluka

Mu 1948 anthu anazindikira kuti mbalame za takahe zikanalipobe. Mbalamezi siziuluka

Ku New Zealand kuli nyama komanso zachilengedwe zambiri. Ndipo ndi dziko lokhali padziko lonse lapansi lomwe lili ndi mitundu yambiri ya mbalame zomwe siziuluka. Kumapezekanso mtundu winawake wa abuluzi otchedwa tuatara, omwe umatha kukhala ndi moyo mpaka zaka 100. Nyama zoyamwitsa za m’dzikoli ndi monga mitundu yochepa ya mileme komanso nsomba zikuluzikulu ngati anangumi ndi ma dolphin.

A Mboni za Yehova akhala akulalikira ku New Zealand kwa zaka pafupifupi 120. Amaphunzitsa anthu Baibulo m’zinenero pafupifupi 19 kuphatikizapo zinenero za ku Polynesia ngati Chinuweya, Chirarotonga, Chisamowa ndi Chitongani.

Amaori akuvina

Amaori akuvina atavala zovala zachikhalidwe chawo

KODI MUKUDZIWA?

Dzina lakuti New Zealand linachokera ku dzina lakuti Zeeland lomwe ndi dera linalake la ku Netherlands. Dzina lakuti Maori kapena kuti Aotearoa limatanthauza “Dziko Lokhala ndi Mtambo Woyera Komanso Wautali.”

Ngakhale kuti anthu ambiri a ku New Zealand amalankhula Chingelezi, chinenero cha Chimaori chayambanso kugwiritsidwa ntchito moti ayamba kuchiphunzitsa m’masukulu. Webusaiti yovomerezeka ya Mboni za Yehova ya jw.org imapezekanso m’Chimaori.

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU: 4.7 MILIYONI

  • LIKULU: WELLINGTON

  • DERA: KU NORTH ISLAND KUMAPHULIKA CHIPHALAPHALA CHOCHOKERA PANSI PANTHAKA KOMANSO KULI AKASUPE A MADZI OTENTHA. KU SOUTH ISLAND KULI MADZI AMBIRI OUNDANA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena