Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g21 No. 3 tsamba 6-7
  • Zimene Zamoyo Zimatiuza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Zamoyo Zimatiuza
  • Galamukani!—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Pali Chamoyo Chimene Si Chodabwitsa?
    Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri
  • Linapangidwa Kuti Likhale Kosatha
    Galamukani!—1995
  • Mafunso Awiri Omwe Tiyenera Kudziwa Mayankho Ake
    Galamukani!—2015
  • Kodi Kuyang’anitsitsa Zinthu Zosaoneka Kumavumbula Chiyani?
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—2021
g21 No. 3 tsamba 6-7
Mkati mwa selo la yisiti.

Selo la yisiti ndi logometsa kwambiri. Lili ndi DNA komanso limagaya chakudya chomwe chimathandiza kuti lipitirizebe kukhala ndi moyo.

Zimene Zamoyo Zimatiuza

Zamoyo zimene timaona zimakula, zimayenda, zimaswana ndipo zimakongoletsa dziko lathuli. Panopa anthu amadziwa zinthu zambiri zokhudza zamoyo kuposa kale. Koma kodi zamoyo zimatiuza chiyani zokhudza chiyambi chake? Taganizirani zotsatirazi:

Zamoyo zimaoneka kuti zinachita kupangidwa. Zinthu zamoyo zinapangidwa ndi tinthu tina ting’onoting’ono totchedwa maselo. Selo lililonse limachita zinthu zambirimbiri kuti zinthu zamoyo zipitirizebe kukhala ndi moyo komanso kuti ziswane. Zimenezi zimachitika ngakhale ndi zamoyo zina zomwe ndi zazing’ono kwambiri. Mwachitsanzo, taganizirani za yisiti amene amagwiritsidwa ntchito mu zinthu ngati mandasi kuti afufume, yemwe ndi kanthu kakang’ono kwambiri. Selo la yisiti silogometsa kwambiri poyerekezera ndi selo limene limakhala m’thupi mwa munthu. Ngakhale zili choncho palokha limachita zinthu modabwitsa kwambiri. Mu selo lililonse, mumakhala DNA. Selo lililonse limagaya chakudya chimene chimathandiza kuti selolo lipitirizebe kukhala ndi moyo. Ngati chakudya chake chayamba kuchepa, selolo limasiya kuchita zinthu zina ndipo limakhala ngati lagona. N’chifukwa chake yisiti amatha kusungidwa kwa nthawi yaitali, n’kudzagwiritsidwanso ntchito bwinobwino.

Asayansi akhala akufufuza za maselo a yisiti kwa zaka zambiri n’cholinga choti adziwe zokhudza maselo a anthu. Komatu pali zambiri zimene sazimvetsa. Pulofesa wina dzina lake Ross King wa ku yunivesite ya Chalmers ku Sweden, ananena kuti: “Pali akatswiri ochepa omwe angamafufuze zinthu zonse zomwe timafunikira kuti tidziwe mmene zinthu ngati yisiti zimagwirira ntchito.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti selo la yisiti lizigwira ntchito mogometsa chonchi, kapena linachita kulengedwa?

Moyo umachokera ku zinthu zamoyo. DNA imapangidwa ndi timamolekyu ting’onoting’ono totchedwa manyukiliyotaidi. Selo lililonse la munthu lili ndi manyukiliyotaidi okwana 3.2 biliyoni. Timamolekyu timeneti, tinayalidwa mu ndondomeko yapadera kuti selo lizitha kupanga mapulotini komanso timadzi tinatake.

Asayansi amanena kuti ngati manyukiliyotaidi atati aziyalana mwaokha pofuna kupanga DNA, pa maulendo mathililiyoni ambirimbiri amene angayese kuchita zimenezi, zingatheke mwina ulendo umodzi wokha. Zimenezi zikusonyeza kuti n’zosatheka kuti manyukiliyotaidi apange DNA mwaokha.

Zoona zake n’zakuti asayansi sanapangepo chinthu chamoyo kuchokera ku chinthu chopanda moyo.

Anthufe ndi apadera. Monga anthu, tili ndi makhalidwe amene amatithandiza kuti tizisangalala kwambiri ndi moyo kuposa chamoyo chilichonse. Tili ndi maluso osiyanasiyana, timakhala bwino ndi anthu ena komanso timasonyezana chikondi. Timatha kumva kakomedwe ka zakudya, fungo, timaphokoso komanso timatha kuona mitundu yosiyanasiyana ya zinthu. Timakonza mapulani a zinthu zam’tsogolo komanso timafufuza cholinga cha moyo.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti tikhale ndi makhalidwe amenewa chifukwa chakuti ndi ofunika kuti tizitha kukhala ndi moyo komanso kuberekana? Kapena kodi zimasonyeza kuti moyo ndi mphatso yochokera kwa Mlengi wachikondi?

Iyi ndi loboti yotchedwa Adam, inapangidwa kuti iziona zokhudza maselo a yisiti

Lobotiyi ndi yaikulu ngati minibasi yaing’ono. Ili ndi firiji, manja, makamera, masensa komanso makompyuta 4. Lobotiyi inapangidwa kuti izichita kafukufuku wovuta wokhudza maselo a yisiti, ndipo yakhaladi ikukwanitsa kuchita zimenezi payokha popanda kuthandizidwa kwenikweni ndi anthu.

Katswiri wasayansi waima pafupi ndi loboti yotchedwa Adam yomwe inapangidwa kuti iziona zokhudza maselo a yisiti.

Ngati mukanauzidwa kuti lobotiyi inangokhalapo yokha popanda woipanga, kodi mukanakhulupirira? N’zokayikitsa. Komatu zomwe lobotiyi imachita, sizingafikepo pa zimene selo la yisiti limachita, lomwenso si selo logometsa kwambiri. Ndiye ngati loboti inachita kupangidwa ndi winawake, kuli bwanji selo?

Onani zitsanzo zochititsa chidwi zosonyeza kuti zamoyo zinachita kulengedwa. Fufuzani nkhani komanso mavidiyo a mutu wakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?” pa jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena