Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 6 tsamba 27-30
  • Mphunzitsi Wamkuru Anawatumikira Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mphunzitsi Wamkuru Anawatumikira Ena
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Mphunzitsi Waluso Anatumikira Anthu Ena
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Anawaphunzitsa Kudzichepetsa pa Pasika Womaliza
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Chifukwa Chake Yesu Anali Mphunzitsi Waluso
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana Ndi Aphunzitsi Anga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 6 tsamba 27-30

Mutu 6

Mphunzitsi Wamkuru Anawatumikira Ena

KODI mumakondwera pamene munthu wina akuchitirani inu kanthu kena?—Eya, anthu ena amakondwera pamene munthu wina awachitiranso iwo kanthu kena. Tonsefe timakondwera. Mphunzitsi Wamkuruyo anachidziwa chimenecho, ndipo iye masiku onse anali kumawachitira anthu zinthu. Iye anati: ‘Ndinadza, osati kuti nditumikiridwe, koma kutumikira.’—Mateyu 20:28.

Chotero, ngati ife tikufuna kukhala ngati Mphunzitsi Wamkuruyo, kodi nchiani chimene ife tiyenera kuchichita?—Ife tiyenera kuwatumikira ena. Tiyenera kuwachitira iwo zinthu zabwino.

Nzoona, anthu ambiri samachita chimenechi. Kunena zoona, anthu ochuruka masiku onse amawafuna ena kuwatumikira iwo. Pa nthawi ina ngakhale atsatiri a Yesu analingalira motere. Ali yense anafuna kukhala wofunika kopambana.

Yesu anadziwa kuti sikunali koyenera kaamba ka iwo kuganizira motere. Chotero, tsiku lina iye anawapatsa iwo phunziro limene iwo sakanaliiwala konse.

Pamene iwo analinkudya pamodzi, Yesu ananyamuka kuchokera pa thebulo. Iye anatenga beseni losambira ndi kuikamo madzi. Pamene iwo anali kuyang’ana, Yesu anapita kwa ali yense wa iwo, nawerama ndi kutsuka mapazi ao. Ndiyeno iye anawapukuta mapazi ao ndi taulo. Tangoganizirani za chimenecho! Bwanji ngati inuyo mukanakhalapo ndipo Yesu anawatsuka mapazi anu? Kodi inuyo mukanamva bwanji?—

Atsatiri ache sanalingalire kuti kunali koyenera kwa Mphunzitsi Wamkuruyo kuwatumikira iwo m’njira imeneyi. Iwo anachita manyazi. Kunena zoona, mmodzi wa iwo sanafune kumlola Yesu kumchitira iye utumiki wodzichepetsa umenewu. Koma Yesu ananena kuti kunali kofunika kaamba ka iye kuuchita uwo.

Ife kawirikawiri sitimatsukana mapazi lero lino. Koma kunali kofala kukuchita uko pamene Yesu anali pa dziko lapansi. Kodi mukuchidziwa chifukwa chache?—

Eya, m’dziko limene iwo anakhala, anthu anali kubvala nkhwawira (sandasi) ku mapazi ao. Chotero pamene iwo anali kuyenda pa miseu yapfumbi, mapazi ao anakutidwa ndi pfumbi. Kunali kukoma mtima kuwatsuka mapazi apfumbi a munthu amene analowa m’nyumba kudzacheza.

Koma nthawi imeneyi palibe mmodzi wa atsatiri a Yesu anadzipereka kuwatsuka mapazi a ena. Chotero Yesu anakuchita uko yekha. Mwa kumachita chimenechi, Yesu anawaphunzitsa atsatiri ache phunziro lofunika. Iwo anafunikira kuliphunzira phunziro limeneli. Ndipo ilo liri phunziro limene ife tifunikira lero lino kuliphunzira.

Kodi mukuchidziwa chimene chiri phunziro limenelo?—Yesu atakhalanso pa malo ache pa thebulolo, iye anafotokoza: ‘Kodi mukuchizindikira chimene ndinakuchitirani? Inu mumandicha ine “Mphunzitsi” ndi “Ambuye,” ndipo inu muli kulondola. Ngati ine, Mphunzitsi ndi Ambuye wanu, ndinawatsuka mapazi anu, pamenepotu inu muyenera kutsukana mapazi.’—Yohane 13:2-14.

Panopo Mphunzitsi Wamkuruyo anasonyeza kuti iye anawafuna atsatiri ache kutumikirana. Iye sanawafune iwo kuganizira kokha ponena za iwo eni. Iye sanafune kuti iwo aganizire kuti iwo anali ofunika kwambiri kuti ena masiku onse ayenera kuwatumikira iwo. Iye anawafuna iwo kukhala ofunitsitsa kutumikira ena.

Kodi limenelo silinali phunziro labwino kwambiri?—Kodi inuyo mudzakhala ngati Mphunzitsi Wamkuruyo ndi kuwatumikira anthu ena?—Ife tonse tingathe kuwachitira ena zinthu.

Sikuli kobvuta kuwatumikira anthu ena. Ngati inu muyang’anitsitsa, mudzapeza zinthu zambiri zimene inu mungathe kuwachitira anthu ena.

Tsopano ganizirani kuti: Kodi pali kanthu kena kali konse kamene inu mungathe kuchita kuwathandiza amai wanu? Inu mukudziwa kuti amakuchitirani zinthu zambiri ndi ena onse a m’banjamo. Kodi mungathe kuwathandiza iwo?—Bwanji osawafunsa iwo?—

Mwinamwache inu mungathe kulinganiza thebulo banjalo lisanadye. Kapena mwinamwache inu mungathe kutolera pamodzi mbale zakuda banjalo litatha kudya. Ana ena amaturutsa kunja zinyalala tsiku liri lonse. Chiri chonse chimene inu mungathe kuchita, chidzakhala kutumikira ena, monga momwedi Yesu anachitira.

Kodi muli ndi aphwanu ndi alongwanu achichepere amene inu mungathe kuwatumikira?—Kumbukirani kuti, Yesu, Mphunzitsi Wamkuruyo, anawatumikira ngakhale atsatiri ache. Mwa kumawatumikira aphwanu ndi alongwanu achicheperewo, inu mudzakhala mukumamtsanzira Yesu.

Kodi nchiani chimene mungawachitire iwo? Kodi mungathe kuganizira chiri chonse?—Mwinamwache inu mungathe kuwathandiza iwo kuphunzira kuziika pa malo ao zidole zao pamene iwo atha kusewera. Kapena mwinamwache inu mungathe kuwathandiza iwo kukonzekera kupita kogona. Iwo adzafikira pa kukukondani kaamba ka kumazichita zinthu zimenezi, monga momwedi atsatiri a Yesu anamkondera iye.

Mu sukulu, namonso, inu mungathe kuwatumikira anthu ena. Ngati munthu wina agwetsa mabukhu ache, kukakhala kukoma mtima kwa inu kumthandiza iye kuwatolera iwo. Inu mungadzipereke kumpukutira mphunzitsi wanu bolodi, kapena kumchitira iye kanthu kena. Ngakhale kumagwira chitseko kuti chikhale chotseguka kaamba ka munthu wina kuli utumiki wokoma mtima.

Nthawi zina mudzapeza kuti anthu sadzatithokoza kaamba ka kumawatumikira iwo. Kodi mukuganiza kuti chimenechi chiyenera kutiletsa ife kuchita zabwino?—Ai! Anthu ambiri sanamthokoze Yesu kaamba ka nchito zache zabwino. Koma chimenecho sichinamletse iye kumachita zabwino.

Chotero tiyeni tisaleke konse kumawatumikira anthu. Tiyeni masiku onse tichitsatire chitsanzo cha Yesu.

(Kaamba ka malemba oonjezereka onena za kumawathandiza anthu ena, werengani Aroma 15:1, 2, Miyambo 3:27, 28 ndi Agalatiya 6:2.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena