Chimene Chinanenedweratu Ponena za Nthawi Yathu ndi M’Tsogolo
Zochitika zonenedweratu ndi Baibulo kaamba ka nthawi yathu zakwaniritsidwa. Kumene’ku kumakupatsani maziko okhalira ndi chidaliro champhamvu m’zimene Malemba Oyera amanena ponena za mtendere? Kodi munadziwa kuti Baibulo limaneneratu zaka chikwi za ulamuliro wa zaka chikwi wa Yesu Kristu umene’wu? Kodi mukufuna kuoneratu madalitso amene udzadzetsa? Pamenepo pezani ndi kuwerenga bukhu lakuti Choonadi Chimene Chimatsogolera ku Moyo Wamuyaya.
Bukhu limene’li limafotokoza’nso zochitika zodabwitsa zonenedweratu kaamba ka nthawi yathu, monga momwe zikupezekera m’Baibulo pa Mateyu chaputala cha makumi awiri mphambu zinai ndi makumi awiri mphambu zisanu. Olongosoledwa ndiwo mafanizo olosera a Yesu Kristu a anamwali khumi, matalente, ndi nkhosa ndi mbuzi. M’mene iwo akugwirizanira ndi m’tsogolo kukulongosoledwa bwino lomwe. Bukhu iri la chikuto cholimba la masamba 192 lidzatumizidwa kwa inu litalipiriridwa kale pa positi pa 25c zokha.
Ngati mungafune kuti wina akufikireni ku nyumba kwanu kudzakambitsirana nanu mafunso a Baibulo, lemberani kalata ku Watchtower ku keyala yoperekedwa pansipa.