Chidziwitso cha pa nthawi yake kaamba ka Ang’ono ndi Akulu
Uthenga wa Baibulo umaphatikizamo mitu ya nkhani yosiyana-siyana yochuluka imene ikulongosoledwa m’mabukhu a ukulu wokhoza kulowa m’thumba a masamba 192 otsatirapo’wa. Inu mukupemphedwa kuitanitsa mabukhu ali onse amene mukufuna, ndipo’nso makope a Mbiri Yabwino Yokusangalatsani oonjezereka amene mungafune kaamba ka mabwenzi anu, pa 35c liri lonse, litalipiridwiratu pa positi, ku iri yonse ya maofesi a pafupi nanu kwambiri a Watch Tower Society olembedwa pa tsamba lotsatirapo’li.
● Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo. Bukhu loti makolo awerenge ndi ana ang’ono kwambiri, kuwaphunzitsa malamulo a khalidwe labwino oyenera okhalira ndi moyo.
● Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Lingakuthandizeni ndi banja lanu kumvetsetsa bwino ziphunzitso zazikulu za Baibulo.
● Mtendere Weni-weni ndi Chisungiko—Zochokera ku Magwero Otani? Limalongosola zobvuta zoyang’anizana ndi mtundu wa anthu, mankhwala ndi miyezo ya Baibulo kaamba ka moyo wokhutiritsa.
Ndipo’nso, Mboni za Yehova mokondwa zidzayankha mafunso anu a Baibulo pa nyumba panu kapena pa King’idomu Holo yao ya kwanuko.