Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
Kabuku aka kasindikizidwa kukuthandizani kudziŵa amene anapanga dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zilipo. Mudzaphunziranso kuti Mulungu, amene anapanga dziko lapansi, ali ndi dzina. Tidzalongosolanso chifukwa chake Mulungu anapanga munthu ndi mmene mungasangalalire ndi moyo pa dziko lapansi pano kosatha.
Tikukhulupirira kuti zithunzi zambirizo zidzakuthandizani kuona bwino kwambiri zinthu zimenezi m’maganizo. Kuti mupindule kopambana, muyenera kuŵerenga malemba a m’Baibulo amene aikidwa pambali pa zochuluka za zithunzizo. Mwa kutero, mudzadziŵerengera nokha ena a malonjezo abwino a Mulungu amene ali m’Baibulo ndi zimene Mulungu akunena kuti muyenera kuchita kuti mulandire kukwaniritsidwa kwa malonjezo ameneŵa.
Mungafunenso kugwiritsira ntchito kabukuka kukuthandizani kuthandiza anthu ena. Ngati muli ndi ana, mungakagwiritsire ntchito kuwathandiza kuphunzira za Mulungu. Ngati mumakhala m’dziko limene achikulire ambiri ali osakhoza kuŵerenga, inu mungagwiritsire ntchito zithunzi kuwathandiza kumvetsetsa zifuno za Mulungu kotero kuti iwo, nawonso, athandize anansi awo.
Moona mtima tikuyembekezera kuti kuphunzira chidziŵitso ichi kudzakutsegulirani njira yolandirira madalitso ambiri, ngakhale kusonyeza ena mmene angakhalire ndi moyo kosatha pano pa dziko lapansi.