Mutu wa Buku Lino/Tsamba la Ofalitsa
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
Anthu mamiliyoni ambiri ali ndi chidziwitso chamaziko cha ziphunzitso za Baibulo. Koma kuti apeze chisangalalo chokwanira cha kukhala ndi mbali m’kulambiridwa kogwirizana kwa Mulungu wowona, afunikira kupita patsogolo ku uchikulire Wachikristu. Bukhu lino lalinganizidwira kuthandiza anthu onse otero kukulitsa ndi kuzamitsa luntha lawo la Mawu a Mulungu ndi kuwagwiritsira ntchito mokwanira kotheratu m’miyoyo yawo.
—Afalitsi