“Pitiriza Kutsatira Zimene Unaphunzira”
Mtumwi Paulo analemba mawu amenewa kwa Timoteyo, amene anali wachinyamata. (2 Timoteyo 3:14) Pamene mwawerenga buku lino, mwadziwa zinthu zambiri zabwino zimene Mulungu wakonzera anthu amene amamukonda. Koma muyenera kupitiriza kupita patsogolo mwauzimu. Anthu a Mboni za Yehova adzakhala okondwa kukuthandizani kuchita zimenezi, ngati simunayambe kale kuthandizidwa mwanjira imeneyi. Ngati mukufuna kudziwa zambiri, kapena ngati mukufuna kuti munthu wa Mboni za Yehova azibwera kunyumba kwanu kudzaphunzira nanu Baibulo kwaulere, ingolembani kalata kwa Mboni za Yehova pogwiritsa ntchito adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali m’munsiwa.