Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 57
  • Kuchitira Chifundo Okanthidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchitira Chifundo Okanthidwa
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Kumvera Chifundo Aumphaŵi
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Yesu Anachiritsa Mtsikana Komanso Munthu Wogontha
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Muli ndi “Mtima Wa Kristu”?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mmene Kulumala Konse Kudzathere
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 57

Mutu 57

Kuchitira Chifundo Okanthidwa

PAMBUYO pakudzudzula Afarisi kaamba ka miyambo yawo yodzikondweretsa, Yesu akuchoka limodzi ndi ophunzira ake. Mudzakumbukira kuti, sikale kwambiri, kuti kuyesayesa kwake kuti achoke limodzi nawo kukapuma pang’ono kunadodometsedwa pamene makamu anampeza. Tsopano, ndi ophunzira ake, akuchoka kumka ku zigawo za Turo ndi Sidoni, makilomitala ambiri chakumpoto. Mwachiwonekere uwu ndiwo ulendo wokha umene Yesu akupanga ndi ophunzira ake kulumpha malire a Israyeli.

Atapeza nyumba yokhalamo, Yesu akuchititsa kuti kudziŵike kuti iye safuna kuti munthu aliyense adziŵe kumene iwo ali. Komabe, ngakhale m’gawo losakhala la Aisrayeli limeneli iye sakubisika. Mkazi wina Wachigiriki, wobadwira kuno ku Foinike wa Suriya akumpeza nayamba kupempha kuti: “Mundichitire ine chifundo, Ambuye, Mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiŵanda.” Komabe, Yesu, sakuyankha mawu alionse.

Potsirizira pake, ophunzira ake akuuza Yesu kuti: “Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu.” Pofotokoza chifukwa chimene akumnyalanyazira, Yesu akuti: “Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israyeli.”

Komabe, mkaziyo sakuleka. Iye akuyandikira kwa Yesu nagwada pamaso pake. Akumchonderera kuti, “Ambuye, ndithangateni ine.”

Mtima wa Yesu uyenera kukhala utasonkhezeredwa chotani nanga ndi kuchonderera kwamphamvu kwa mkaziyo! Komabe, kachiŵirinso iye akusonyeza thayo lake loyambirira, kutumikira anthu a Mulungu a Israyeli. Panthaŵi imodzimodziyo, mwachiwonekere kuti ayese chikhulupiriro chake, iye akusonyeza lingaliro la tsankho la Ayuda kulinga kwa anthu a mitundu ina, akumati: “Sichabwino kutenga mkate wa ana ndi kuuponyera tiagalu.”

Mwa kamvekedwe ka liwu lake kosonyeza chifundo ndi chisonyezero chankhope, ndithudi Yesu akusonyeza malingaliro ake achifundo kwa osakhala Ayuda. Iye akufeŵetsa ngakhale kuyerekezera Amitundu ndi agalu mwa kuwatcha iwo “tiagalu” kapena nkhanda. Mmalo mwakukhumudwa ndi mawuwo, mkaziyo akuyankha mawu a Yesu osonyeza tsankho la Ayuda napereka lingaliro lodzichepetsa lakuti: “Etu, Ambuye, pakuti tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye wawo.”

“Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndichachikulu,” Yesu akuyankha motero. “Chikhale kwa iwe monga momwe wafunira.” Ndipo zikutero! Pamene abwerera kunyumba kwake, akupeza mwana wake wamkaziyo pakama, atachira kotheratu.

Kuchokera kuchigawo chakugombe cha Sidoni, Yesu ndi ophunzira ake akumuka modutsa dzikolo, kumagwero a Mtsinje wa Yordano. Mwachiwonekere iwo akuwoloka Yordano penapake kumtunda kwa Nyanja ya Galileya ndi kuloŵa m’chigawo cha Dekapoli kummaŵa kwa nyanjayo. Kumeneko iwo akukwera phiri, koma makamu akuwapeza nabweretsa kwa Yesu opunduka awo, opuŵala, akhungu, ndi osalankhula, ndi ambiri amene ali ndi nthenda zamitundumitundu ndi opuwala. Iwo akuwaika pamapazi a Yesu, ndipo akuwachiritsa. Anthuwo akuzizwa, pamene akuwona osalankhula akulankhula, opunduka akuyenda, ndipo akhungu akuwona; ndipo akutamanda Mulungu wa Israyeli.

Yesu akupereka chisamaliro chapadera kwa munthu mmodzi amene ali wogontha ndi wosalankhula. Kaŵirikaŵiri anthu ogontha amagwidwa ndi manyazi mofulumira, makamaka m’khamu la anthu. Yesu angakhale atawona chinthenthe chenicheni cha mwamuna ameneyu. Chotero Yesu mokoma mtima akumtengera pambali kuchoka m’khamulo. Pamene iwo ali okha, Yesu akusonyeza zimene adzamchitira. Iye akuika zala zake m’makutu a munthuyo ndipo, pambuyo pakulavula malovu, akhudza lilime lake. Pamenepo, atagadamira kumwamba, Yesu akuusa moyo kwambiri nati: “Tatseguka.” Pamenepo, mphamvu zakumva za munthuyo zikubwezeretsedwa, ndipo iye ali wokhoza kulankhula mozoloŵereka.

Pamene Yesu wachita machiritso ambiri ameneŵa makamuwo akuyamikira. Iwo akuti: “Wachita iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.” Mateyu 15:21-31; Marko 7:24-37.

▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu sakuchiritsa nthaŵi yomweyo mwana wamkazi wa mkazi Wachigiriki?

▪ Pambuyo pake, kodi nkuti kumene Yesu akutengera ophunzira ake?

▪ Kodi ndimotani mmene Yesu mokoma mtima akuchitira ndi munthu wogontha amene sangalankhule?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena