Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 59
  • Kodi Yesu Kwenikweni Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yesu Kwenikweni Ndani?
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali Yesu?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Mwana wa Munthu Ndi Ndani?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Anakhalabe Wokhulupirika Panthawi Yovuta
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Anakhalabe Wokhulupirika pa Nthawi Yovuta
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 59

Mutu 59

Kodi Yesu Kwenikweni Ndani?

PAMENE ngalaŵa imene anakweramo Yesu ndi ophunzira ake ikukocheza pa Betsaida, anthu ena akudza ndi munthu wakhungu kwa iye ndi kumpempha kukhudza munthuyo kuti amchiritse. Yesu akutsogolera munthuyo mwakumugwira padzanja napita naye kunja kwa mudzi ndipo, atamthira malovu m’maso mwake, akufunsa kuti: “Uwona kanthu kodi?”

“Ndiwona anthu,” munthuyo akuyankha motero, “pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.” Ataika manja m’maso mwa munthuyo, Yesu akubwezeretsa kuwona kwake kotero kuti iye akuwona bwino lomwe. Kenako Yesu akutumiza munthuyo kwawo ndi kumlangiza kusaloŵa mumzinda.

Yesu tsopano akunyamuka ndi ophunzira ake kumka kumudzi wa Kaisareya wa Filipi, kumpoto kwenikweni kwa Palestina. Uli mtunda wautali, wofola chifupifupi makilomitala 48, kupita kumalo okongola a Kaisareya wa Filipi, okwezeka mamitala 350 kuchokera pamtunda wanyanja. Ulendowo mwinamwake umatenga masiku angapo.

Adakali m’njira, Yesu akupatuka payekha kukapemphera. Pangotsala miyezi pafupifupi isanu ndi inayi kapena khumi imfa yake isanafike, ndipo akudera nkhaŵa ponena za ophunzira ake. Ambiri aleka kale kumtsatira. Ena mwachiwonekere ali osokonezeka ndi olefulidwa maganizo chifukwa chakuti iye adakana zoyesayesa za anthu kumpanga mfumu ndi chifukwa chakuti, pamene anatokosedwa ndi adani ake, sanapereke chizindikiro chochokera kumwamba kutsimikizira uchifumu wake. Kodi atumwi ake akukhulupiriranji ponena za zimene iye ali? Pamene akudza kumene iye akupempherera, Yesu akufunsa kuti: “Makamuwo a anthu anena kuti ndine yani?”

“Ena ati, Yohane Mbatizi,” iwo akuyankha motero, “koma ena, ati Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.” Inde, anthu akulingalira kuti Yesu ali mmodzi wa amuna ameneŵa woukitsidwa kwa akufa!

“Koma inu mutani kuti ine ndine yani?” akufunsa motero Yesu.

Mwamsanga Petro akuyankha: “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”

Atasonyeza kuvomereza yankho la Petro, Yesu akuti: “Ndiponso ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pathanthwe iri ndidzakhazika mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa [Hade] sadzaulaka uwo.” Panopa Yesu choyamba akulengeza kuti adzamanga mpingo ndi kuti ngakhale imfa siidzaika muukapolo ziŵalo zake pambuyo pa moyo wawo wokhulupirika padziko lapansi. Ndiyeno akuuza Petro kuti: “Ndidzakupatsa mafungulo a ufumu wakumwamba.”

Motero Yesu akuvumbula kuti Petro adzalandira mwaŵi wapadera. Ayi, Petro sakupatsidwa malo oyamba pakati pa atumwi, kaya kupangidwa kukhala maziko a mpingowo. Yesu iye mwini ndiye Thanthwe pa limene mpingo wake udzamangidwa. Koma Petro adzapatsidwa mfungulo zitatu zotsegulira, kunena kwake titero, mwaŵi kumagulu a anthu kuloŵa Muufumu wakumwamba.

Petro akagwiritsira ntchito mfungulo yoyamba pa Pentekoste wa 33 C.E. kusonyeza Ayuda olapa chimene ayenera kuchita kuti apulumutsidwe. Akagwiritsira ntchito mfungulo yachiŵiri posapita nthaŵi yaitali pambuyo pake kutsegulira Asamariya okhulupirira mwaŵi wakuloŵa Muufumu wa Mulungu. Ndiyeno, mu 36 C.E. iye akagwiritsira ntchito mfungulo yachitatu kutsegulira Akunja osadulidwa, Korneliyo ndi mabwenzi ake, mwaŵi umodzimodziwo.

Yesu akupitiriza kukambitsirana ndi ophunzira ake. Iye akuwalefula maganizo mwa kuwauza za zowawa ndi imfa zimene adzayang’anizana nazo posachedwa mu Yerusalemu. Polephera kuzindikira kuti Yesu adzaukitsidwira kumoyo wakumwamba, Petro akutengera Yesu pambali. “Dzichitireni chifundo, Ambuye,” iye akutero. “Sichidzatero kwa inu ayi.” Atapotoloka, Yesu akuyankha kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa ine, chifukwa susamalira za Mulungu, koma za anthu.”

Mwachiwonekere, ena kusiyapo atumwiwo akuyenda limodzi ndi Yesu, chotero tsopano akuwaitana ndi kuwafotokozera kuti sikudzakhala kopepuka kukhala wotsatira wake. “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga,” iye akutero, “adzikanize yekha, nanyamule [mtengo wozunzirapo] wake nanditsata ine. Pakuti yense wakufunafuna kupulumutsa moyo wake adzautaya; ndipo yense wakutaya moyo wake chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwino, adzaupulumutsa.”

Inde, ngati akayenerera chiyanjo chake, otsatira Yesu ayenera kukhala olimbika mtima ndi odzipereka. Iye akufotokoza kuti: “Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha ine, ndi cha mawu anga mumbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene iye adzafika nawo angelo ake oyera, muulemelero wa Atate wake.” Marko 8:22-38; Mateyu 16:13-28; Luka 9:18-27.

▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu ali wodera nkhaŵa ponena za ophunzira ake?

▪ Kodi anthu akulingalira kuti Yesu ali yani?

▪ Kodi ndimfungulo zotani zimene zikupatsidwa kwa Petro, ndipo ziyenera kugwiritsiridwa ntchito motani?

▪ Kodi ndichiwongolero chotani chimene Petro akulandira, ndipo nchifukwa ninji?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena