Mutu 76
Kudyera Limodzi ndi Mfarisi
ATATHA Yesu kuyankha otsutsawo amene akukayikira magwero a mphamvu yake ya kuchiritsa munthu amene sanakhoza kulankhula, Mfarisi wina akumuitana kukadyera naye limodzi. Asanayambe kudya, Afarisi amadziloŵetsa m’mwambo wa kusamba manja awo kufikira m’zigongono. Iwo amachita zimenezi chakudya chisanakhale ndi pambuyo pake ndipo ngakhale mkati mwake. Ngakhale kuti mwambowo suumaswa lamulo la Mulungu lolembedwa, umawonjezera zoposa zimene Mulungu amafuna m’nkhani ya chiyero cha mwambo.
Pamene Yesu alephera kusunga mwambowo, womchereza wakeyo akudabwa. Ngakhale kuti kudabwa kwake sikungasonyezedwe mwamawu, Yesu akukuzindikira ndipo akuti: “Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma mkati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa. Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapanganso mkati mwake?”
Motero Yesu akuvumbula chinyengo cha Afarisi amene mwamwambo amasamba manja awo koma nalephera kutsuka mitima yawo pa zoipa. Iye akulangiza kuti: “Patsani mphatso yachifundo za mkatimo; ndipo wonani, zonse ziri zoyera kwa inu.” Kupatsa kwawo kuyenera kusonkhezeredwa ndi mtima wachikondi, osati ndi chikhumbo cha kudziwonetsera kwa ena ndi kudziyerekezera kwawo kukhala olungama.
“Tsoka inu, Afarisi!” Yesu akupitiriza motero, “chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.” Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli chimawafuna kuti apereke chakhumi kapena mbali ya khumi, ya zokolola za m’munda. Timbewu tonunkhira ndi timbewu tokometsa chakudya ziri zomera zazing’ono kapena timasamba togwiritsiridwa ntchito kununkhiritsa chakudya. Mosamalitsa Afarisiwo amaperekadi chakhumi cha timasamba tating’ono timeneti, koma Yesu akuwatsutsa kaamba ka kunyalanyaza chinthu chofunika kwambiri cha kusonyeza chikondi, kuchitira chifundo, ndi kukhala wodzichepetsa.
Powadzudzula mowonjezereka, Yesu akuti: “Tsoka inu, Afarisi! chifukwa mukonda mipando yaulemu m’masunagoge, ndi kulankhulidwa m’misika. Tsoka inu! chifukwa muli ngati manda osawoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pawo sadziŵa.” Kunyansa kwawo nkosawonekera. Chipembedzo cha Afarisi chiri ndi kudziwonetsera kwa kunja koma chosayenerera mkati! Nchozikidwa pachinyengo.
Pomvetsera kukudzudzulidwa koteroko, loyala wina, mmodzi wa anthu odziŵa kwambiri Chilamulo cha Mulungu, akudandaula kuti: “Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.”
Yesu akupatsanso mlandu akatswiri ameneŵa Achilamulo, akumati: “Tsoka inunso, achilamulo inu! chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi. Tsoka inu! chifukwa mumanga za pamanda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha.”
Akatundu amene Yesu akutchulawo ndiwo miyambo yapakamwa, koma maloyala ameneŵa sakanyamula konse ngakhale lamulo limodzi laling’ono kuti zipepukire anthuwo. Yesu akuvumbula kuti iwo amavomereza ngakhale kuphedwa kwa aneneri, ndipo iye akuchenjeza kuti: “Mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno; kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zakariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.”
Dziko la anthu okhoza kuomboledwa linayambira pakubadwa kwa ana a Adamu ndi Hava; motero, Abele anakhalako ‘chiyambi cha kukhazika kwa dziko lapansi.’ Pambuyo pa kuphedwa kwachiwawa kwa Zekariya, gulu la nkhondo la Asuri linafunkha Yuda. Koma Yesu akuneneratu za kufunkha kwina koipitsitsa kwa mbadwo wake chifukwa cha kuipa kwake kwakukulu. Kufunkha kumeneku kukuchitika pafupifupi zaka 38 pambuyo pake, mu 70 C.E.
Popitiriza kutsutsa kwake, Yesu akuti: “Tsoka inu, achilamulo! chifukwa munachotsa chimfungulo cha nzeru; inu simunaloŵamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkuloŵa.” Akatswiri a Chilamulowo ali ndi thayo la kufotokozera anthu Mawu a Mulungu, kumasulira tanthauzo lake. Koma iwo akulephera kuchita zimenezi ndipo ngakhale kuchotsera anthuwo mwaŵi wa kuzindikira.
Afarisi ndi akatswiri a malamulowo akwiya naye Yesu chifukwa cha kuwaulula. Pamene iye achoka panyumbapo, iwo akuyamba kutsutsana naye mwaukali ndi kumfunsa mafunso ambiri. Iwo akuyesayesa kumtchera msampha mwa kunena kanthu kena kamene iwo angachititse kumgwira. Luka 11:37-54; Deuteronomo 14:22; Mika 6:8; 2 Mbiri 24:20-25.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akudzudzula Afarisi ndi akatswiri a Chilamulo?
▪ Kodi ndiakatundu otani amene maloyala akuika pa anthu?
▪ Kodi ‘chiyambi cha kukhazika kwa dziko lapansi’ chinali liti?