Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • la mutu 9 tsamba 28-31
  • Sangalalani ndi Moyo Wokhutiritsa—Tsopanolino ndi Kwamuyaya!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sangalalani ndi Moyo Wokhutiritsa—Tsopanolino ndi Kwamuyaya!
  • Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
  • Nkhani Yofanana
  • “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
    “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
  • Dalirani Yehova Kuti Adzakwaniritsa Chifuno Chake
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Dziko Latsopano Lili Pafupi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
la mutu 9 tsamba 28-31

Mutu 9

Sangalalani ndi Moyo Wokhutiritsa—Tsopanolino ndi Kwamuyaya!

1, 2. Kodi muyenera kuchitanji kuti mukhale ndi moyo wokhutiritsa?

ABRAHAMU, mwamuna wotchuka pa chikhulupiriro wa m’mbiri ya m’Baibulo, anasiya moyo wosangalatsa mumzinda wotukuka wa Uri. Atakhala kanthaŵi mu Harana, moyo wake wonse unakhala wa machokachoka, wokhala m’mahema, wopanda nyumba yachikhalire. (Genesis 12:1-3; Machitidwe 7:2-7; Ahebri 11:8-10) Komabe, kunalembedwa kuti: “Abrahamu anamwalira, nafa m’ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri.” (Genesis 25:8) Kodi chinapangitsa moyo wake kukhala wokhutiritsa choncho n’chiyani? Iye sanali nkhalamba wamba imene inali yokhutira pakama wofera, chabe chifukwa chakuti anakwaniritsa zambiri m’moyo ayi. Pambuyo pake Abrahamu anadzatchedwa “bwenzi la Mulungu” chifukwa cha chikhulupiriro chake chapadera mwa Mulungu. (Yakobo 2:23; Yesaya 41:8) Ubale watanthauzo umene Abrahamu anapalana ndi Mlengi wake ndi umene unapangitsa moyo wake kukhala wokhutiritsa.

2 Monga momwe Abrahamu anachitira zaka 4,000 zapitazo, inunso mutha kukhala ndi moyo watanthauzo ndi wokhutiritsa lerolino, ngati mupalana ubwenzi ndi Mulungu. Mwina mungadabwe kumva za kukhala bwenzi la Mlengi wa chilengedwe chonse, komatu n’zotheka. Motani? Mufunikira kum’dziŵa ndi kum’konda. (1 Akorinto 8:3; Agalatiya 4:9) Ubwenzi woterowo ndi Mlengi ungapangitse moyo wanu kukhala watanthauzo ndi wokhutiritsa.

3, 4. N’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kukhala ndi moyo wogwirizana ndi njira za Mulungu?

3 Kwa aja amene akufuna kulandira nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, Yehova wapereka malangizo ake okhalira ndi moyo wachimwemwe. (Yesaya 48:17) Kumbukirani, Adamu anapandukira Mulungu mwa kudzisankhira yekha zabwino ndi zoipa. Ngakhale kuti Yehova kudzera mwa nsembe ya dipo ya Mwana wake anagula banja la anthu onse, ndi kuwapatsa njira yowalanditsira ku ukapolo wa uchimo ndi imfa, munthu aliyense payekha ayenera kulandira dipolo ndi kusiya kudziikira miyezo yakeyake ya zabwino ndi zoipa. Tiyenera kugonjera malamulo ndi malangizo amene Mulungu amapereka kwa aja amene amalandira nsembe ya dipo ya Yesu.

4 Pamene mupitiriza kuphunzira Baibulo ndi kugwiritsa ntchito malangizo operekedwa mmenemo, ndithudi mudzazindikira phindu lake la muyezo wa Mulungu wa zabwino ndi zoipa. (Salmo 19:7-9) Mudzakhudzidwa mtima ndi kunena kwa Mulungu mmene ananenera Mose, mneneri wa Yehova kuti: “Tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziŵitsetu njira zanu, kuti ndikudziŵeni.” (Eksodo 33:13; Salmo 25:4) Baibulo limapereka mfundo zachikhalidwe zokuthandizani kudutsa m’mavuto a mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino. (2 Timoteo 3:1) Chiyamikiro chanu chidzakula, ndipo chidzakuthandizani kum’dziŵa bwino Yehova ndipo chidzalimbitsa ubwenzi wanu ndi iye.

5. Kodi chofunika n’chiyani kuti moyo ukhale wokhutiritsa kwenikweni?

5 Abrahamu anamwalira “m’ukalamba wake wabwino,” koma malinga ngati wina amwalira, moyo umakhalabe waufupi kwambiri. Ngakhale tingakalambe chotani, chikhumbo chokhala ndi moyo n’chachibadwa mwa tonsefe. Zili choncho chifukwa chakuti “[Mulungu] waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.” (Mlaliki 3:11) Ngakhale tikadzakhala ndi moyo wamuyaya, sitidzathabe kumvetsa zonse zimene Yehova analenga. Zimene tingaone, kuphunzira, ndi kusangalala nazo, mwa ntchito zodabwitsa za Yehova, zilibe polekezera!—Salmo 19:1-4; 104:24; 139:14.

6, 7. Kodi mikhalidwe yabwino ndi moyo wosatha zidzapezeka motani?

6 Simungasirire kudzakhala ndi moyo wosatha ngati dziko lapansi lingadzakhale ndi mavuto ngati tikuwaona leroŵa. Komabe, imeneyo isakhale nkhaŵa yanu. Baibulo limalonjeza kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Mawu akuti “miyamba yatsopano” amatanthauza boma latsopano lakumwamba—Ufumu wa Mulungu, umene udzalamulira dziko lonse lapansi. “Dziko latsopano” ndilo mtundu watsopano wa anthu omvera ulamuliro wa Ufumu umenewo. Kuti zimenezi zitheke, posachedwa Yehova adzachitapo kanthu pothana ndi aja amene “akuwononga dziko.”—Chivumbulutso 11:18; 2 Petro 3:10.

7 Kodi ndi posachedwa chotani? Monga mbali ya “chizindikiro cha . . . mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” Yesu Kristu anatchulanso nkhondo pakati pa mitundu ya anthu, “njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti,” “miliri,” ndi “kuchuluka kwa kusayeruzika.” (Mateyu 24:3-13; Luka 21:10, 11; 2 Timoteo 3:1-5) Kenako iye analosera kuti: “Pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.” (Luka 21:31) Ndithudi, nthaŵi yoti Yehova awononge anthu oipa ikufika mofulumira.a

8. Kodi Yehova adzaonetsa motani chidwi chake kwa aja amene anafa?

8 Pambuyo pa “tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,” pamene Yehova adzasesa padziko lapansi zoipa zonse, dziko lapansi lathuli lidzasanduka paradaiso. (Chivumbulutso 16:14, 16; Yesaya 51:3) Panthaŵiyo, “olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Koma bwanji za aja amene anamwalira? Yesu anati: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.” (Yohane 5:28, 29) Yehova, amene ali ndi chidwi ndi munthu wina aliyense, adzaukitsa aja amene akugona mu imfa. Asayansi angayese kubadwitsa anthu ofanana kudzera m’njira ya m’maselo, popanda kugonana kwa mwamuna ndi mkazi, koma Mlengi sangachite kuvutika ndi kubadwitsa anthu mwa njira imeneyo. Iye amatha kukumbukira mbali iliyonse ya munthu aliyense woyenera kuwomboledwa komanso kumuukitsa kuti akhalenso ndi moyo. Inde, muli ndi chiyembekezo chodzaonananso m’paradaiso wa padziko lapansi ndi okondedwa anu omwe anafa!

9. Kodi ulamuliro wa Mulungu udzachita zotani kwa anthu pa dziko lapansi?

9 Kodi moyo udzakhala wotani m’Paradaiso? Dziko lapansi lidzadzaza ndi amuna ndi akazi achisangalalo otamanda Mlengi wawo mogwirizana. “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24; 54:13) Palibenso munthu amene adzakhala ndi vuto lililonse la maganizo kapena malingaliro. Onse adzakhala ndi chakudya cha mwana alirenji ndipo adzasangalala pogwira ntchito zatanthauzo zogwirizana ndi cholinga cha Mulungu. (Salmo 72:16; Yesaya 65:23) Adzasangalala pokhala pamtendere ndi nyama, pamtendere ndi anthu anzawo, koma choposa zonse, adzakhala pa “mtendere ndi Mulungu.”—Aroma 5:1; Salmo 37:11; 72:7; Yesaya 11:6-9.

10. Kodi muyenera kuchitanji kuti mudzakhale ndi moyo wokhutiritsa m’Paradaiso?

10 Kodi muyenera kuchitanji kuti mudzaloŵe nawo m’Paradaiso ameneyo ndi kuti mudzapeze nawo moyo wokhutiritsa mokwanira? Yesu Kristu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Choncho pitirizani kuphunzira kuti mum’dziŵe Yehova ndi Yesu Kristu, ndi kutinso mudziŵe zimene Mulungu amazifuna kwa inu. Mukatero mudzam’kondweretsa Yehova Mulungu, ndipo zimenezo zidzapangitsa moyo wanu kukhala wokhutiritsa kopambana.

[Mawu a M’munsi]

a Mutha kudziŵa zambiri za ulosi umenewu poŵerenga mutu 9 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 28]

Mukhoza kukhala ndi moyo wokhutiritsa ngati mupalana ubwenzi ndi Mulungu

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi mungapangitse moyo wanu kukhala wokhutiritsa kwambiri koposa ngakhale uja wa Abrahamu?

[Chithunzi patsamba 29]

“Mundidziŵitsetu njira zanu”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena