Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kp tsamba 3-5
  • Kodi Dzikoli Likuloŵera Kuti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Dzikoli Likuloŵera Kuti?
  • Dikirani!
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chiwonongeko cha Dziko Chonenedweratucho Chidzadza Liti?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Kodi Anthu Angadzetse Mtendere Wosatha ndi Chisungiko?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Ulosi wa Baibulo Umene Mwawona Ukukwaniritsidwa
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Masiku Otsiriza
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Dikirani!
kp tsamba 3-5

Kodi Dzikoli Likuloŵera Kuti?

Mavuto aakulu ndiponso zochitika zoipa kwambiri zovuta kuzimvetsa zikuchitika tsiku lililonse padziko lapansi. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

KUTETEZEKA KWA ANTHU: Mabomba aphulitsidwa m’misika. Aphunzitsi ndi ana asukulu aomberedwa ku sukulu. Makanda abedwa pamene makolo awo anangoyang’ana kumbali kwa kanthaŵi kochepa. Azimayi ngakhalenso azibambo okalamba achitidwa chifwamba dzuŵa likuswa mtengo.

ZOCHITIKA M’CHIPEMBEDZO: Matchalitchi akuthandiza magulu otsutsana pa nkhondo. Atsogoleri achipembedzo aimbidwa mlandu wopulula fuko la anthu. Ansembe achita zachiwerewere ndi ana; tchalitchi chibisa nkhaniyo. Opita ku tchalitchi akuchepa; matchalitchi agulitsidwa.

CHILENGEDWE: Nkhalango zadulidwa kuti achitirepo zamalonda. Anthu osauka amaliza mitengo pofuna nkhuni. Madzi a pansi pa nthaka aipitsidwa, si abwino kumwa. Nsomba ziwonongedwa chifukwa cha zonyansa zochokera m’mafakitale ndi njira zina zamakono zophera nsomba. Mpweya ukutsamwitsa chifukwa choipitsidwa.

KUPEZA ZOFUNIKA PAMOYO: Ndalama zimene munthu amapeza pachaka kum’mwera kwa Africa n’zochepa kwambiri. Dyera la akuluakulu a makampani ligwetsa makampani, n’kuchititsa anthu ambirimbiri kukhala pa ulova. Chinyengo chichititsa anthu amene anagula nawo makampani kutaya ndalama zawo zonse.

KUPEREŴERA KWA ZAKUDYA: Anthu pafupifupi 800,000,000 padziko lonse amagona ndi njala nthaŵi zonse.

NKHONDO: Anthu opitirira 100,000,000 anafa chifukwa cha nkhondo m’zaka za m’ma 1900. Pali zida za nyukiliya zotha kuwononga anthu onse padziko lapansi maulendo ambirimbiri. Nkhondo zapachiweniweni. Uchigawenga ufalikira pa dziko lonse lapansi.

MILIRI NDI MATENDA ENA: Kuyambira mu 1918, fuluwenza ya ku Spain inapha anthu 21,000,000. Edzi tsopano yasanduka “mliri wowononga kwambiri m’mbiri yonse ya anthu.” Matenda a kansa ndi a mtima amabweretsa chisoni kwa anthu padziko lonse lapansi.

Musangoona nkhani iliyonse payokha. Kodi nkhanizo n’zosakhudzana ndi zochitika zina? Kapena kodi nkhani zimenezi ndi mbali ya zochitika za padziko lonse zimene zili ndi tanthauzo lenileni?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]

Kodi Mulungu Amatiganiziradi?

Chifukwa chokhumudwa ndi zochitika zoipa kwambiri zovuta kuzimvetsa kapena chifukwa choferedwa kapena kutayikidwa katundu, anthu ambiri amadzifunsa chifukwa chimene Mulungu saloŵererapo kuti aletse zinthu ngati zimenezo.

Mulungu amatiganiziradi. Amatipatsa malangizo odalirika ndi chithandizo chenicheni panopa. (Mateyu 11:28-30; 2 Timoteo 3:16, 17) Wayala maziko othetseratu chiwawa, matenda, ndi imfa. Zimene wakonza zimasonyeza kuti amaganizira, osati anthu a mtundu umodzi wokha, koma anthu a mitundu, mafuko, ndi zinenero zonse.—Machitidwe 10:34, 35.

Kodi za Mulungu Zimatikhudza Kwambiri Bwanji? Kodi mukumudziŵa Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi dzina lake ndani? Kodi zolinga zake n’zotani? Iye amayankha mafunso ameneŵa m’Baibulo. M’Baibulomo amatiuza zimene akuchita kuti athetse chiwawa ndiponso matenda ndi imfa. Kuti tidzapindule ndi zimenezi, kodi tifunika kuchita chiyani? Tifunika kuphunzira za iye ndi zolinga zake. Kodi tingayembekezere kupindula ndi zimene wakonza ngati sitimukhulupirira? (Yohane 3:16; Ahebri 11:6) M’pofunikanso kuti tizichita zimene amafuna. (1 Yohane 5:3) Kodi za Mulungu zimakukhudzani kwambiri moti mumafuna kuchita zimenezo?

Kuti timvetsetse chifukwa chimene Mulungu amalolera zinthu zimene zikuchitika masiku anozi kuchitika, tifunika kumvetsetsa nkhani yofunika kwambiri. Baibulo limafotokoza nkhani imeneyi, yomwe taifotokoza pa tsamba 15 la kabuku kano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena