Chikuto Chakumbuyo
Bukuli likuthandizani kuyankha mafunso onena za:
KUSIRIRA MNYAMATA KAPENA MTSIKANA
Malangizo abwino ndi ofunika. Buku lachiwiri la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, lili ndi malangizo abwino amene angakuthandizeni. Buku loyamba linasindikizidwa m’zinenero zoposa 80 ndipo mabuku oposa 40 miliyoni anafalitsidwa. Mofanana ndi buku loyamba, m’buku lino muli zimene achinyamata ambiri padziko lonse ananena atafunsidwa mafunso pankhani zosiyanasiyana. Malangizo a m’Baibulo anawathandiza kwambiri ndipo tikukhulupirira kuti inunso akuthandizani.
“Tenga nzeru, tenga luntha.”—Miyambo 4:5.