Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp2 tsamba 50
  • Chitsanzo Chabwino—Yosefe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Chabwino—Yosefe
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Ndingachitirenji Choipa Chachikulu N’kuchimwira Mulungu?’
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Ankasamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Kapolo Amene Ankamvera Mulungu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • “Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
yp2 tsamba 50

Chitsanzo Chabwino​—Yosefe

Yosefe anakumana ndi chiyeso chachikulu. Mkazi wa mbuye wake ankamunyengerera mobwerezabwereza kuti agone naye. Tsiku lina mkaziyo anayesa kumunyengerera, koma Yosefe sanatengeke. Iye anayankha motsimikiza kuti: ‘Ndingachitirenji choipa chachikulu chimenechi, ndi kuchimwira Mulungu?’ Mkaziyo atalimbikira mpaka kufika pomugwira, Yosefe sanachite manyazi kuthawa, kutuluka m’nyumbamo. Yosefe anasonyeza kuti anali munthu wamakhalidwe abwino.—Genesis 39:7-12.

Mwina inunso mungakumane ndi munthu amene angakunyengerereni kuti mugone naye. Kudziletsa pakokha sikokwanira kuti mukane kuchita zimenezo. Choyamba, muyenera kufunitsitsa kukondweretsa Mlengi wanu, Yehova Mulungu. Mofanana ndi inu, Yosefe anali ndi chilakolako cha kugonana. Koma anaona kuti si bwino kuchimwira Mlengi wake chifukwa chotsatira chilakolako chake. Inunso muyenera kukhala wotsimikiza kuti kuchita khalidwe lililonse lodetsa n’kuchimwira Mulungu ndipo kumabweretsa mavuto. Choncho, yesetsani kuti mukhale wamakhalidwe abwino ngati Yosefe.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena