Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp2 tsamba 193
  • Chitsanzo Chabwino—Hezekiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Chabwino—Hezekiya
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Nkhani Yofanana
  • Anatipatsa Ufulu Wosankha
    Nsanja ya Olonda—2010
  • “Anapitiriza Kumamatira Yehova”
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
yp2 tsamba 193

Chitsanzo Chabwino​—Hezekiya

Hezekiya anakhala mfumu ya Yuda ali ndi zaka 25 zokha. Imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri m’moyo wake. Kodi iye akanakhala mfumu yotani? Kodi akanatengera chitsanzo choipa cha bambo ake, Mfumu Ahazi? Iye anali wampatuko ndipo sanafune kulapa mpaka imfa yake. Mfumu Ahazi analimbikitsa kulambira konyenga komanso anafika mpaka popereka nsembe m’bale wake wa Hezekiya, pomuotcha paguwa la nsembe la mulungu wonyenga. (2 Mbiri 28:1-4) Koma Hezekiya sanafune kutengera chitsanzo choipa cha bambo ake, n’kulephera kutumikira Yehova. Iye sanachite zinthu zoipa zimene abambo ake anachita, m’malo mwake ‘anaumirirabe kwa Yehova.’—2 Mafumu 18:6.

Kodi bambo kapena mayi anu amanyoza kulambira koona? Kodi iwo ali ndi makhalidwe enaake oipa? Ngati ndi choncho, inu simuyenera kutengera makhalidwe awowo. Hezekiya sanalole kuti moyo wake usokonezeke ndi khalidwe loipa la panyumba pawo. Ndipo anakhala mfumu yabwino kwambiri, moti “atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda.” (2 Mafumu 18:5) Mofanana ndi Hezekiya, nanunso mungakhale wamakhalidwe abwino ngakhale mutakulira m’banja lamakhalidwe oipa. Mungachite motani zimenezi? Mungatero mwa ‘kuumirirabe kwa Yehova.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena