Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp2 tsamba 257
  • Chitsanzo Chabwino—Davide

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Chabwino—Davide
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Nkhani Yofanana
  • Mfumu Davide Anali Wokonda Nyimbo
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingasungire Nyimbo m’Malo Ake?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhalira Kumvetsera Nyimbo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kusangalala ndi Nyimbo—Nchiyani Chimene Chiri Mfungulo?
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
yp2 tsamba 257

Chitsanzo Chabwino​—Davide

Davide ankakonda nyimbo. Iye anali ndi luso lopeka komanso kuimba nyimbo. Iye ankakonzanso yekha zida zake zoimbira. (2 Mbiri 7:6) Chifukwa cha luso la Davide, mfumu ya Isiraeli inamuitanitsa kuti azikaimba ku nyumba yake. (1 Samueli 16:15-23) Davide anavomera, koma sanalole kuti zimenezi zimuchititse kukhala wonyada, komanso kuti azingokhalira kuimba kokhakokha. M’malo mwake iye anagwiritsa ntchito luso lakelo kutamanda Yehova.

Kodi inuyo mumakonda nyimbo? Mwina simungakhale ndi luso loimba ngati Davide, komabe mungatsanzire chitsanzo chake. Kuti muchite zimenezi, musamangokhalira kumvetsera nyimbo nthawi zonse ndipo musalole kuti nyimbo zikusokonezeni maganizo n’kumachita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Koma muzimvetsera nyimbo n’cholinga choti musangalale. Luso lopeka komanso kusangalala ndi nyimbo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Yakobe 1:17) Davide ankagwiritsa ntchito luso limeneli kusangalatsa Yehova. Inunso mungathe kuchita zimenezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena