Nyimbo 20
Dalitsani Msonkhano Wathu!
Losindikizidwa
1. Pamsonkhanowu Yehova,
Tipempha m’tidalitse.
Ndifetu oyamikira,
Mzimu ukhale nafe.
2. M’tithandize polambira,
M’tipatse Mawu anu.
M’tiphunzitse kulalika,
Tikhale achikondi.
3. Mudalitse misonkhano,
Mutipatse mtendere.
Mawu ndi zochita zathu
Zikulemekezeni.
(Onaninso Sal. 22:22; 34:3; Yes. 50:4.)