Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp1 tsamba 97
  • Chitsanzo Chabwino—Yobu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Chabwino—Yobu
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Nkhani Yofanana
  • Yobu Anapirira—Nafenso Tingatero!
    Nsanja ya Olonda—1994
  • “Mudamva za Chipiriro cha Yobu”
    Nsanja ya Olonda—2006
  • “Yembekezera Yehova”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Mwamuna Wachitsanzo Chabwino Amene Anavomera Kum’langiza
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
yp1 tsamba 97

Chitsanzo Chabwino​—Yobu

Pa nthawi ina, zinthu zinasintha kwambiri pa moyo wa Yobu. Choyamba, ziweto zake zonse zinafa. Chachiwiri, ana ake onse anamwalira. Chachitatu, anadwala matenda aakulu. Zonsezi zinachitika motsatizanatsatizana komanso modzidzimutsa. Kenako atathedwa nzeru ananena kuti: “Ineyo ndikunyansidwa ndi moyo wanga.” Pofotokoza mmene ankamvera, ananenanso kuti: “Ndachita manyazi kwambiri ndipo ndadzazidwa ndi mavuto.” (Yobu 10:1, 15) Ngakhale pamene ankakumana ndi mavuto onsewo, Yobu anakana kuchimwira Mlengi wake. (Yobu 2:10) Mavuto amene anakumana nawo pa moyo wake sanamusinthe. N’chifukwa chake Yobu ali chitsanzo chabwino pa nkhani yopirira.

N’kutheka kuti nanunso mukakumana ndi mavuto mukhoza ‘kunyansidwa ndi moyo wanu.’ Koma potengera Yobu, musalole kuti mavuto amene mukukumana nawo akusintheni n’kuyamba kuchita zinthu mokayikira potumikira Yehova Mulungu. Yakobo analemba kuti: “Monga mmene mukudziwira, anthu amene anapirira timawatcha odala. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa, mwaona kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Yehova anathandiza Yobu, inunso adzakuthandizani.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena