Mkati Mwachikuto
Okondedwa Achinyamata Nonse,
Atate wanu wakumwamba, Yehova Mulungu, amakukondani kwambiri ndipo amafuna kuti muzisangalala. Koma mwina mungamadzifunse kuti, ‘Kodi mmene zinthu zilili panopa n’zothekadi kukhala wosangalala?’ Limeneli ndi funso labwino chifukwatu panopa tikukumana ndi mavuto ambiri pa moyo wathu. Tsiku lililonse timakumana ndi mavuto amene akhoza kutilepheretsa kukhala osangalala. Komatu Atate wathu wachikondi akufuna kutithandiza. Mawu ake ali ndi malangizo ofunikira amene angatithandize kulimbana ndi mavuto amene timakumana nawo. Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa kalekale, malangizo ake ndi othandizabe masiku ano ngati mmene analili othandiza pa nthawi imene linkalembedwa.—Salimo 119:98, 99; 2 Timoteyo 3:16, 17.
Takulemberani bukuli chifukwa chakuti timakukondani kwambiri. Tikufuna kuti muzikhala osangalala komanso kuti zinthu zizikuyenderani bwino. Kuti zimenezi zitheke, tikukulimbikitsani kuti muwerenge buku lonseli komanso muzifufuzamo mfundo zothandiza mukakumana ndi mavuto. Cholinga china cha bukuli ndi kukulimbikitsani kuti muzilankhulana momasuka ndi makolo anu. Tikukhulupirira kuti muwerenga ndiponso kukambirana zigawo zina za bukuli limodzi ndi makolo anu. Yesetsani kuphunzira zambiri pa nzeru zimene makolo anu ali nazo komanso pa zimene akumana nazo pa moyo wawo.
Tikukufunirani zabwino zonse,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova