Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yc phunziro 4 tsamba 10-11
  • Anasangalatsa Bambo Ake Komanso Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anasangalatsa Bambo Ake Komanso Yehova
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Yofanana
  • Ankakondedwa Ndi Mulungu Komanso Anzake
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Lonjezo la Yefita
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yehova Amadalitsa Anthu Okhulupirika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Zimene Yefita Analonjeza
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Phunzitsani Ana Anu
yc phunziro 4 tsamba 10-11

PHUNZIRO 4

Anasangalatsa Bambo Ake Komanso Yehova

Kodi Yefita akumulonjeza chiyani Yehova?

Chaka chilichonse anzake a mwana wa Yefita ankapita kuchihema kukamuona

Kodi wamuona mtsikana ali pachithunzipa?—Ameneyu ndi mwana wa Yefita. Baibulo silitiuza dzina lake koma tikudziwa kuti anasangalatsa bambo ake komanso Yehova. Tiye tikambirane za mtsikanayu komanso bambo ake.

Yefita anali munthu wabwino ndipo nthawi zambiri ankaphunzitsa mwana wakeyu za Yehova. Anali munthu wamphamvu komanso mtsogoleri wabwino. Ndiyeno Aisiraeli anamupempha kuti awatsogolere pokamenya nkhondo.

Yefita anapemphera kwa Mulungu kuti awathandize kupambana nkhondoyo. Iye analonjeza kuti ngati atapambana, adzapereka kwa Yehova munthu amene adzakhale woyamba kumuchingamira pochoka kunkhondoko. Munthu ameneyu akanayenera kukakhala komanso kugwira ntchito ku chihema cha Mulungu kwa moyo wake wonse. Chihema chinali chitenti kumene anthu a nthawi imeneyo ankapitako kukalambira Mulungu. Ndiyeno Yefita anapambanadi nkhondo ija. Kodi ukudziwa munthu amene anali woyamba kudzamuchingamira?—

Anali mwana wake. Yefita anali ndi mwana mmodzi yekhayo ndipo malinga ndi zimene analonjeza zija, anayenera kumupereka kwa Yehova. Yefita anadandaula kwambiri ndi zimenezi. Koma anayenera kumuperekabe chifukwa anali atalonjeza. Nthawi yomweyo, mtsikanayo ananena kuti: ‘Bambo, munalonjeza kwa Yehova ndiye musasinthe zimene munalonjezazo.’

Mwana wa Yefita anachita zimene bambo ake analonjeza ngakhale kuti zinali zovuta

Nayenso mwana wa Yefita anadandaula chifukwa chodziwa kuti akapita kuchihemako sakakhalanso ndi mwayi wokwatiwa komanso kukhala ndi ana. Koma analola kupita chifukwa ankafuna kuti zimene bambo ake analonjeza zichitike ndiponso ankafuna kusangalatsa Yehova. Iye anaona kuti kusangalatsa bambo ake komanso Yehova kunali kofunika kwambiri kuposa kukwatiwa kapena kukhala ndi ana. Ndiyeno mwana wa Yefita anachoka kwawo n’kumakakhala kuchihema kwa moyo wake wonse.

Kodi ukuganiza kuti bambo ake komanso Yehova anasangalala ndi zimene anachitazo?— Inde. Ngati nawenso uzimvera komanso kukonda Yehova, makolo ako ndiponso Yehova adzasangalala nawe kwambiri.

WERENGANI MAVESI AWA

  • Deuteronomo 6:4-6

  • Oweruza 11:30-40

  • 1 Akorinto 7:37, 38

MAFUNSO:

  • Kodi Yefita anali ndani? Nanga analonjeza chiyani?

  • N’chifukwa chiyani zinali zovuta kuti mwana wa Yefita achite zimene bambo ake analonjeza?

  • Kodi mwana wa Yefita ankafunitsitsa kuchita chiyani?

  • Kodi iweyo ungatani kuti ufanane ndi mwana wa Yefita?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena