Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 81 tsamba 190-tsamba 191 ndime 2
  • Ulaliki wa Paphiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulaliki wa Paphiri
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Yesu Anali Mphunzitsi Waluso
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Pitirizani Kuchita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2008
  • “Ndakutchani Mabwenzi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Ulaliki Wotchuka Koposa Onse Operekedwapo
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 81 tsamba 190-tsamba 191 ndime 2
Yesu akulalikira paphiri kwa anthu ambiri

MUTU 81

Ulaliki wa Paphiri

Yesu atasankha atumwi ake 12, anatsika m’phiri n’kupita pamalo amene panasonkhana anthu ambiri. Anthuwo anali ochokera ku Galileya, Yudeya, Turo, Sidoni, Siriya komanso kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano. Anamubweretsera anthu odwala matenda osiyanasiyana komanso amene ankavutitsidwa ndi ziwanda. Yesu anawachiritsa onsewo. Kenako anakhala pansi n’kuyamba kuwaphunzitsa. Anafotokoza zimene munthu angachite ngati akufuna kuti Mulungu akhale mnzake. Yesu anatinso tiyenera kuzindikira kuti timafunika kutsogoleredwa ndi Yehova ndipo tiyenera kuphunzira za iye kuti tizimukonda. Koma ananena kuti sitingakonde Mulungu ngati sitikonda anzathu. Komanso tiyenera kuchitira zabwino aliyense, ngakhale adani athu.

Yesu anati: ‘Kungokonda anzanu si kokwanira. Muyenera kukondanso adani anu komanso muzikhululuka kuchokera pansi pa mtima. Ngati wina wakulakwirani, muzipita kukakambirana naye n’kupepesana. Muzichitira anthu zimene mungafune kuti iwonso akuchitireni.’

Yesu akulalikira paphiri kwa anthu ambiri

Yesu anaperekanso malangizo abwino okhudza chuma. Iye anati: ‘Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi ndalama zambiri. Munthu angathe kukuberani ndalama koma sangakubereni ubwenzi wanu ndi Yehova. Siyani kudandaula kuti: “Mawa tidzadya chiyani, tidzamwa chiyani nanga tidzavala chiyani?” Ganizirani za mbalame. Mulungu amaonetsetsa kuti nthawi zonse zili ndi chakudya chokwanira. Kudandaula sikungapangitse kuti mukhale ndi moyo wautali. Musaiwale kuti Yehova amadziwa zimene mukufunikira.’

Anthuwo anali asanamvepo munthu akulankhula ngati mmene Yesu ankalankhulira. Atsogoleri a chipembedzo anali asanawaphunzitsepo zimenezi. N’chifukwa chiyani Yesu ankatha kuphunzitsa bwino chonchi? Chifukwa choti zonse zimene ankaphunzitsa zinkachokera kwa Yehova.

“Senzani goli langa ndipo lolani kuti ndikuphunzitseni, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa ndipo mudzatsitsimulidwa.”​—Mateyu 11:29

Mafunso: Kodi tingatani kuti Mulungu akhale mnzathu? Kodi Mulungu amafuna kuti tizichitira anthu ena zinthu zotani?

Mateyu 4:24, 25; 5:1-48; 6:19-34; 7:28, 29; Luka 6:17-31

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena