Mawu Oyamba Gawo 6
Aisiraeli atafika m’Dziko Lolonjezedwa ankalambira Mulungu kuchihema. Ansembe ankaphunzitsa Chilamulo ndipo oweruza ndi amene ankatsogolera anthu. Chigawochi chikufotokoza mmene zosankha komanso zochita za munthu zimakhudzira anthu ena. Mwisiraeli aliyense ankafunikira kukonda Yehova komanso anthu ena. Fotokozani mmene zochita za Debora, Naomi, Yoswa, Hana, mwana wamkazi wa Yefita komanso Samueli zinathandizira anthu ena. Tsindikani mfundo yakuti ngakhale anthu a mitundu ina anasankha kugwirizana ndi Aisiraeli chifukwa ankadziwa kuti Mulungu ankawatsogolera. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Rahabi, Rute, Yaeli ndiponso anthu a ku Gibiyoni.