Mawu Oyamba Gawo 10
Yehova ndi Mfumu ya chilengedwe chonse. Iye wakhala akulamulira kuyambira kalekale ndipo sadzasiya. Mwachitsanzo, iye anapulumutsa Yeremiya ataponyedwa m’chitsime kuti afe. Anapulumutsanso Shadireki, Misheki ndi Abedinego m’ng’anjo ya moto ndiponso anapulumutsa Danieli m’dzenje la mikango. Iye anatetezanso Esitere n’cholinga choti apulumutse anthu a mtundu wake. Yehova sadzalola kuti zoipa zizingopitirizabe. Ulosi wonena za chifaniziro chachikulu komanso mtengo waukulu umasonyeza kuti Ufumu wa Yehova udzathetsa mavuto onse ndipo udzalamulira dziko lonse.