Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 20 tsamba 23
  • Mawu Omaliza Abwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mawu Omaliza Abwino
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Mawu Omaliza Ogwira Mtima
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kufotokoza Bwino Malemba
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kuwafika Pamtima Anthu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 20 tsamba 23

PHUNZIRO 20

Mawu Omaliza Abwino

Lemba

Mlaliki 12:13, 14

MFUNDO YAIKULU: Mawu anu omaliza azithandiza anthu kuvomereza zimene aphunzira n’kuyamba kuzigwiritsa ntchito.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Mawu omaliza azikhala ogwirizana ndi mutu wa nkhani yonse. Muzibwereza mfundo zikuluzikulu komanso mutu wa nkhani.

  • Limbikitsani anthu kutsatira zimene aphunzira. Auzeni anthu zoyenera kuchita komanso zifukwa zochitira zinthuzo. Mawu anu omaliza azikhala ochokera mumtima ndipo muziwanena motsimikiza.

  • Mawu omaliza azikhala achidule komanso osavuta. Musatchule mfundo ina yatsopano. Mawu ake angokhala ochepa koma othandiza anthu kudziwa zoyenera kuchita.

    Mfundo yothandiza

    Mukamamaliza nkhani yanu musamalankhule mofulumira ndipo mawu anu asamazirale kumapeto. Ziganizo zomaliza muzizinena ndi mphamvu yosonyeza kuti n’kumapeto.

MU UTUMIKI

M’mawu anu omaliza muzitchula mfundo imene mukufuna kuti munthuyo aziikumbukira. Ngati zinazake zakusokonezani moti mukufunika kungoidula nkhaniyo, malizani ndi mawu olimbikitsa. Ngakhale munthu atakhala wachipongwe muzimuyankha m’njira yoti ulendo wina adzalole kukambirana naye.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena