Chikumbumtima
Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova anapereka chikumbumtima kwa anthu onse?
Onaninso 2Ak 4:2
N’chiyani chingachitikire chikumbumtima cha munthu amene akupitirizabe kuchita zoipa?
Kodi n’zokwanira kumangokhulupirira kuti zimene tikuchita ndi zoyenera?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Mb 18:1-3; 19:1, 2—Mfumu Yehosafati anathandiza Mfumu yoipa Ahabu ndipo Yehova anamukwiyira chifukwa anachita zinthu mopanda nzeru
Mac 22:19, 20; 26:9-11—Mtumwi Paulo anafotokoza kuti nthawi ina ankaganiza kuti kuzunza komanso kupha otsatira a Khristu sikunali kulakwa
Kodi tingatani kuti tiziphunzitsa bwino chikumbumtima?
2Ti 3:16, 17; Heb 5:14
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 24:2-7—Chikumbumtima cha Mfumu Davide chinamuthandiza kuti asachitire zoipa Mfumu Sauli yemwe anali wodzozedwa wa Yehova
Ngakhale kuti anthu ndi ochimwa, kodi angachite chiyani kuti akhale ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu?
Aef 1:7; Ahe 9:14; 1Pe 3:21; 1Yo 1:7, 9; 2:1, 2
Onaninso Chv 1:5
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yes 6:1-8—Yehova anatsimikizira mneneri Yesaya kuti machimo ake akhoza kukhululukidwa
Chv 7:9-14—A khamu lalikulu amatha kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova chifukwa chakuti nsembe ya Khristu imathandiza kuti machimo awo akhululukidwe
N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza chikumbumtima chathu chimene tinachiphunzitsa kutsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu?
Mac 24:15, 16; 1Ti 1:5, 6, 19; 1Pe 3:16
Onaninso Aro 13:5
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 2:25; 3:6-13—Adamu ndi Hava ananyalanyaza chikumbumtima chawo ndipo mapeto ake anachita manyazi chifukwa cholephera kumvera Mulungu
Ne 5:1-13—Bwanamkubwa Nehemiya anayesetsa kuthandiza Ayuda anzake kuti chikumbumtima chawo chiwathandize kumvera malamulo a Mulungu ndi kupewa kupeza phindu mwachinyengo