Kukhumudwa
Kukhumudwa chifukwa choti anthu ena atinenera zoipa
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 8:1-6—Mneneri Samueli anakhumudwa Aisiraeli atakakamira kuti awasankhire mfumu
1Sa 20:30-34—Yonatani anakhumudwa komanso kuchita manyazi bambo ake, Mfumu Sauli atamulusira
Malemba otonthoza:
Onaninso Miy 19:11; Afi 4:8
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:
Sl 55:12-14, 16-18, 22—Ngakhale kuti Mfumu Davide anaukiridwa ndi mnzake wapamtima Ahitofeli, iye anatulira Yehova nkhawa zake ndipo anatonthozedwa
2Ti 4:16-18—Pamene mtumwi Paulo ankaimbidwa mlandu m’khoti, anzake onse anamusiya yekha koma iye anapeza mphamvu atalimbikitsidwa ndi Yehova komanso chifukwa cha chiyembekezo chimene Iye amapereka
Kukhumudwa chifukwa cha zofooka komanso machimo athu
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Sl 51:1-5—Mfumu Davide anamva kupweteka kwambiri mumtima chifukwa cha machimo amene analakwira Yehova
Aro 7:19-24 —Mtumwi Paulo ankadzimvera chisoni chifukwa chakuti anali pa nkhondo yolimbana ndi maganizo ochita zoipa m’malo mochita zabwino
Malemba otonthoza:
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:
1Mf 9:2-5—Ngakhale kuti Mfumu Davide anachita machimo akuluakulu, Yehova amamukumbukira kuti ndi munthu wokhulupirika
1Ti 1:12-16—Mtumwi Paulo anali ndi chikhulupiriro kuti Mulungu amuchitira chifundo ngakhale anachita machimo akuluakulu m’mbuyomu