Kukonda Dziko
Kodi ndi ndani amene akulamulira dzikoli?
Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:
Lu 4:5-8—Satana ananena kuti akhoza kuika Yesu kukhala wolamulira maboma adzikoli ndipo Yesu sanakane kuti Satana ali ndi mphamvu zotha kuchita zimenezi
Kodi n’chiyani chingachitikire ubwenzi wathu ndi Yehova ngati tikufunanso kukonda dzikoli?
Onaninso Yak 1:27
Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:
2Mb 18:1-3; 19:1, 2—Yehova anadzudzula Mfumu Yehosafati chifukwa chopanga mgwirizano ndi Ahabu, mfumu yoipa
Kodi kudziwa mmene Yehova amaonera dzikoli kungatithandize bwanji kuti tizisankha mwanzeru anthu ocheza nawo?
Onani “Anthu Ocheza Nawo”
N’chifukwa chiyani sitimayendera maganizo a dziko pa nkhani ya chuma ndi zinthu zina?
Onani “Kukonda Chuma”
N’chifukwa chiyani sitimayendera maganizo a dzikoli pa nkhani ya kugonana?
N’chifukwa chiyani Akhristu amapewa kulemekeza kwambiri anthu ndi mabungwe?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mac 12:21-23—Yehova anapha Mfumu Herode Agiripa 1 chifukwa choti analola kuti anthu azilambira iyeyo m’malo mwa Mulungu
Chv 22:8, 9—Yohane atayesa kugwadira mngelo, mngeloyo anamuletsa n’kumuuza kuti ayenera kulambira Yehova yekha basi
N’chifukwa chiyani Akhristu sachita nawo ndale kapena kulowerera m’zochitika za dzikoli?
N’chifukwa chiyani Akhristu amakana kuchita zinthu limodzi ndi zipembedzo zina?
N’chifukwa chiyani Akhristu amakana kuyendera mfundo zimene anthu am’dzikoli amayendera?
Lu 10:16; Akl 2:8; 1At 4:7, 8; 2Ti 4:3-5
Onaninso Lu 7:30