Mtima
Kodi timadziwa bwanji kuti Baibulo likamagwiritsa ntchito mawu akuti “mtima,” nthawi zambiri limatanthauza umunthu wathu wamkati, kuphatikizapo maganizo, zolinga, makhalidwe komanso mmene tikumvera?
Sl 49:3; Miy 16:9; Lu 5:22; Mac 2:26
Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:
Lu 9:46-48—Yesu anadzudzula atumwi ake ataona kuti anali ndi mtima wodziona ngati apamwamba
N’chifukwa chiyani timafunika kuteteza mtima wathu?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 6:5-7—Kuipa kwa mtima wa anthu kunachititsa kuti azichita zachiwawa ndipo chifukwa cha zimenezi, Mulungu anabweretsa Chigumula padziko
1Mf 11:1-10—Mfumu Solomo analephera kuteteza mtima wake ndipo anakwatira akazi achilendo, omwe anamuchititsa kuti asiye kutumikira Mulungu wake ndi mtima wonse
Mko 7:18-23—Yesu anafotokoza kuti maganizo oipa amayambira mumtima ndipo angachititse kuti tichite zinthu zomwe Mulungu amadana nazo
Kodi tingateteze bwanji mtima wathu?
Sl 19:14; Miy 3:3-6; Lu 21:34; Afi 4:8
Onaninso Eza 7:8-10; Sl 119:11
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Aef 6:14-18; 1At 5:8—Pofotokoza zida za nkhondo yauzimu, mtumwi Paulo ananena kuti chilungamo, chikhulupiriro komanso chikondi zimateteza mtima wathu wophiphiritsa mofanana ndi mmene chodzitetezera pachifuwa chimatetezera mtima weniweni
Kodi tingadziwe bwanji kuti mtima wathu wophiphiritsa uli ndi vuto?
Onaninso Miy 6:12-14
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Mb 25:1, 2, 17-27—Pa nthawi ina Mfumu Amaziya ankachita zoyenera pamaso pa Mulungu koma sankakonda Yehova ndi mtima wonse. Iye anayamba mtima wodzikuza n’kusiya kutsatira Yehova ndipo pamapeto pake anaphedwa
Mt 7:17-20—Yesu ananena kuti tikakhala ndi mtima woipa tingamachitenso zinthu zoipa
N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi mtima wabwino? Nanga tingatani kuti zimenezi zitheke?
Onaninso Sl 119:97, 104; Aro 12:9-16; 1Ti 1:5
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Mf 20:1-6—Mfumu Hezekiya anali wokhulupirika ndipo ankatumikira Yehova ndi mtima wonse. Choncho atadwala anapempha Yehova kuti amuthandize
Mt 21:28-32—Yesu ananena fanizo losonyeza kuti zimene zili mumtima mwa munthu zimadziwika ndi zimene amachita kuposa zimene wanena kuti adzachita
N’chifukwa chiyani timatonthozedwa tikadziwa kuti Yehova amaona zomwe zili mumtima mwathu?
Onaninso 1Sa 2:3
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 16:1-13—Mneneri Samueli anazindikira kuti kwa Yehova, chofunika si mmene munthu amaonekera koma mtima wake
2Mb 6:28-31—Pemphero la Mfumu Solomo lotsegulira kachisi wa Yehova, linasonyeza kuti Mulungu amadziwa bwino zomwe zili mumtima wathu, ndipo iye amatisamalira potengera zomwe amadziwa zokhudza ifeyo