Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • scl tsamba 33-34
  • Kudzichepetsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudzichepetsa
  • Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
scl tsamba 33-34

Kudzichepetsa

Kodi Yehova amawaona bwanji anthu odzichepetsa komanso odzikuza?

Sl 138:6; Miy 15:25; 16:18, 19; 22:4; 1Pe 5:5

Onaninso Miy 29:23; Yes 2:11, 12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mb 26:3-5, 16-21​—Mfumu Uziya anayamba kudzikuza ndipo anasiya kutsatira Chilamulo cha Mulungu. Atapatsidwa malangizo anakwiya ndipo Mulungu anamukantha ndi khate

    • Lu 18:9-14​—Yesu ananena fanizo losonyeza mmene Yehova amaonera mapemphero a anthu odzikuza ndi odzichepetsa

Kodi Yehova amatani anthu odzichepetsa akalapa mochokera pansi pa mtima?

2Mb 7:13, 14; Sl 51:2-4, 17

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mb 12:5-7​—Mfumu Rehobowamu ndi akalonga a Yuda anadzichepetsa pamaso pa Yehova ndipo Yehova sanawalange

    • 2Mb 32:24-26​—Hezekiya yemwe anali mfumu yabwino anayamba kudzikuza koma Yehova anamukhululukira atadzichepetsa

Kodi kukhala odzichepetsa kungatithandize bwanji?

Aef 4:1, 2; Afi 2:3; Akl 3:12, 13

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 33:3, 4​—Esau anakwiyira kwambiri Yakobo koma Yakobo anasonyeza kudzichepetsa kwakukulu popita kukakumana naye ndipo zimenezi zinathandiza kuti pakati pawo pakhale mtendere

    • Owe 8:1-3​—Woweruza Gidiyoni anauza amuna a ku Efuraimu kuti ndi apamwamba kuposa iyeyo ndipo zimenezi zinathandiza kuti mkwiyo wawo uthe

Kodi Yesu Khristu anaphunzitsa bwanji kuti kukhala odzichepetsa n’kofunika kwambiri?

Mt 18:1-5; 23:11, 12; Mko 10:41-45

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yes 53:7; Afi 2:7, 8​—Mogwirizana ndi zimene aneneri ananeneratu, Yesu anali wodzichepetsa ndipo anali wofunitsitsa kubwera padziko ndiponso kufa imfa yochititsa manyazi komanso yowawa kwambiri

    • Lu 14:7-11​—Yesu anafotokoza nkhani yokhudza kukhala pamalo olemekezeka kuphwando pofuna kutithandiza kuona ubwino wa kudzichepetsa

    • Yoh 13:3-17​—Yesu anasonyeza otsatira ake chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa posambitsa mapazi a atumwi ake

Kodi kuona ena komanso ifeyo mmene Yehova amationera kungatithandize bwanji kukhala odzichepetsa?

Aro 12:3, 16; 1Ak 4:7; Afi 2:3, 4

N’chifukwa chiyani kudzichepetsa kwabodza n’kopanda phindu?

Mt 6:16-18; Akl 2:18, 23

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena