Kufatsa
Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova ndi wofatsa?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Mf 19:12—Pamene Eliya ankavutika maganizo, Yehova anamulankhula mawu “achifatse apansipansi”
Yon 3:10–4:11—Ngakhale kuti Yona analankhula ndi Yehova atakwiya, zimene anamuchitira mokoma mtima zinam’phunzitsa khalidwe la chifundo
Kodi tingasonyeze bwanji kufatsa?
Miy 15:1; Aef 4:1-3; Tit 3:2; Yak 3:13, 17; 1Pe 3:15
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Nu 11:26-29—Mneneri Mose anayankha mofatsa pamene Yoswa anamuuza kuti aletse anthu ena amene ankanenera
Owe 8:1-3—Woweruza Gidiyoni anayankha mofatsa anthu omwe ankafuna kukangana naye