Makolo
Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anayambitsa banja?
Kodi makolo ayenera kuwaona bwanji ana awo?
Onaninso “Ana; Achinyamata”
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 33:4, 5—Yakobo ankaona kuti ana ake ndi madalitso ochokera kwa Yehova
Eks 1:15, 16, 22; 2:1-4; 6:20—Amuramu ndi Yokebedi anabereka Mose ndipo iwo analolera kuika moyo wawo pangozi kuti ateteze mwanayo
Kodi makolo ayenera kuchitira ana awo zinthu zotani?
N’chifukwa chiyani ndi bwino kuphunzitsa ana kuti azimvera Yehova?
Onaninso 2Ti 3:14, 15
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 2:18-21, 26; 3:19 —Makolo a Samueli anapereka mwana wawo kuti azikatumikira kuchihema, komabe iwo ankapita kukamuona komanso kukamupatsa zofunikira; zimenezi zinathandiza kuti akhale munthu wokonda Yehova ndiponso azimutumikira mokhulupirika
Lu 2:51, 52—Yesu anapitirizabe kumvera makolo ake ngakhale kuti iwo sanali angwiro
Kodi makolo angapeze kuti malangizo ophunzitsira ana awo?
De 6:4-9; Aef 6:4; 2Ti 3:14-17
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Owe 13:2-8—Mngelo atauza Manowa kuti mkazi wake adzakhala ndi mwana, iye anapempha Yehova kuti awapatse nzeru za mmene angalerere mwanayo
Sl 78:3-8—Yehova amafuna kuti makolo aziphunzitsa ana awo mfundo za m’Baibulo
N’chifukwa chiyani ana amene akulira m’banja lokonda Mulungu amatha kusankha kusatumikira Yehova?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Kodi makolo ayenera kuyamba liti kuphunzitsa ana awo zimene Mulungu amafuna kuti azichita?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
De 29:10-12, 29; 31:12; Eza 10:1—Aisiraeli akasonkhana pamodzi kuti aphunzire zokhudza Yehova, ankakhala limodzi ndi ana awo
Lu 2:41-52—Chaka chilichonse, Yosefe ndi Mariya ankatenga ana awo kuphatikizapo Yesu popita kuchikondwerero cha Pasika kukachisi wa ku Yerusalemu
Kodi makolo ayenera kutsatira zitsanzo ziti pamene akufuna kuteteza ana awo kwa anthu amene angawachitire nkhanza?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Eks 19:4; De 32:11, 12—Yehova anadziyerekezera ndi chiwombankhanga chimene chimanyamula, kuteteza komanso kusamalira ana ake
Yes 49:15—Yehova analonjeza kuti adzasamalira komanso kuteteza atumiki ake kuposa mmene mayi woyamwitsa amasamalirira mwana wake wakhanda
Mt 2:1-16—Satana ankafuna kupha Yesu ali wakhanda potsogolera anthu okhulupirira nyenyezi kwa Mfumu Herode, koma Yehova anateteza Mwana wake pouza Yosefe kuti athawire ku Iguputo
Mt 23:37—Yesu anasonyeza kuti ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu ake mofanana ndi mmene nkhuku yathadzi imatetezera ana ake powabisa m’mapiko
N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuphunzitsa ana awo nkhani zokhudza kugonana?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Le 15:2, 3, 16, 18, 19; De 31:10-13—Chilamulo cha Mose chinkanena mosapita m’mbali nkhani zokhudza kugonana ndipo Yehova analamula kuti ana azimvetsera nawo Chilamulochi chikamawerengedwa mokweza
Sl 139:13-16—Wamasalimo Davide anatamanda Yehova chifukwa cha mmene thupi la munthu linalengedwera modabwitsa komanso m’njira yoti anthu azitha kubereka ana
Miy 2:10-15—Kudziwa zinthu komanso nzeru zochokera kwa Yehova zingatiteteze kwa anthu oipa komanso achinyengo
N’chifukwa chiyani makolo ayenera kulangiza kapena kuphunzitsa ana awo mwachikondi?
Miy 13:24; 29:17; Yer 30:11; Aef 6:4
Onaninso Sl 25:8; 145:9; Akl 3:21
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Sl 32:1-5—Yehova anapereka chilango kwa Mfumu Davide chifukwa cha tchimo lomwe anachita komabe analimbikitsidwa atadziwa kuti Yehova amakhululukira anthu omwe alapa kuchokera pansi pa mtima
Yon 4:1-11—Mneneri Yona analankhula kwa Yehova mopsa mtima komanso mopanda ulemu; komabe Yehova anamulezera mtima pofuna kumuphunzitsa kuti Iye ndi wachifundo
N’chifukwa chiyani tinganene kuti makolo amasonyeza chikondi akamapereka chilango kwa ana awo?
Onaninso Miy 15:32; Chv 3:19