Kulalikira Uthenga Wabwino
N’chifukwa chiyani Akhristu oona onse amauza ena zimene amakhulupirira?
Kodi Yesu anatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani yolalikira?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Lu 4:42-44—Yesu ananena kuti anabwera padziko lapansi kudzagwira ntchito yolalikira
Yoh 4:31-34—Yesu anafotokoza kuti ntchito yolalikira inali ngati chakudya chake
Kodi ndi amuna audindo okha mumpingo amene ayenera kumagwira ntchito yolalikira uthenga wabwino?
Sl 68:11; 148:12, 13; Mac 2:17, 18
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Mf 5:1-4, 13, 14, 17—Kamtsikana ka Chiisiraeli kanauza mkazi wa Namani zokhudza Elisa mneneri wa Yehova
Mt 21:15, 16—Yesu anatsutsa ansembe aakulu ndi alembi pamene ankaletsa ana kumutamanda m’kachisi
Kodi oyang’anira angasonyeze bwanji chitsanzo chabwino polalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa ena mumpingo kuti azilalikira?
Kodi Yehova ndi Yesu amatithandiza bwanji pamene tikugwira ntchito yolalikira?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mac 16:12, 22-24; 1At 2:1, 2—Ngakhale kuti mtumwi Paulo ndi anzake ankachitidwa zachipongwe, Mulungu anawathandiza kupitiriza kulalikira molimba mtima
2Ak 12:7-9—Mtumwi Paulo yemwe anali mlaliki wakhama, anali ndi “minga m’thupi,” yomwe mwina inali matenda a m’thupi; koma Yehova anamupatsa mphamvu kuti apitirize kugwira ntchito yolalikira
Kodi ndi ndani amene amapatsa Akhristu ufulu komanso mphamvu zolalikira?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tiziphunzitsa ena kuti azitha kulalikira komanso kuphunzitsa
Mko 1:17; Lu 8:1; Aef 4:11, 12
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yes 50:4, 5—Asanabwere padzikoli, Mesiya analandira maphunziro kuchokera kwa Yehova Mulungu
Mt 10:5-7—Ali padzikoli, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake moleza mtima kugwira ntchito yolalikira
Kodi tiyenera kuona bwanji ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino?
Kodi Akhristu amamva bwanji akamagwira ntchito yolalikira?
Kodi timalankhula zinthu ziti tikamalalikira uthenga wabwino?
N’chifukwa chiyani timauza anthu ena mosabisa zokhudza ziphunzitso zabodza?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mko 12:18-27—Yesu anagwiritsa ntchito Malemba posonyeza Asaduki kuti ankalakwitsa posakhulupirira za kuuka kwa akufa
Mac 17:16, 17, 29, 30—Mtumwi Paulo anafotokozera anthu a ku Atene zifukwa zosonyeza kuti n’kulakwa kulambira mafano
Kodi timatani pogwira ntchito yolalikira?
N’chifukwa chiyani timalalikira kulikonse kumene kuli anthu?
Yoh 18:20; Mac 16:13; 17:17; 18:4
Onaninso Miy 1:20, 21
Pamene tikugwira ntchito yolalikira, n’chifukwa chiyani timafunika kuleza mtima ndiponso kupirira?
Kodi uthenga wabwino umakhudza bwanji anthu amene ali ndi chidwi?
N’chifukwa chiyani Mkhristu aliyense afunika kugwiritsa ntchito mpata uliwonse umene ali nawo kuti alalikire?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yoh 4:6, 7, 13, 14—Ngakhale kuti Yesu anatopa, koma analalikirabe uthenga wabwino kwa mzimayi wa Chisamariya pachitsime
Afi 1:12-14—Ngakhale kuti mtumwi Paulo anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chake, anagwiritsa ntchito mpata umene anali nawo kuti alalikire komanso kulimbikitsa ena
Kodi tiziyembekezera kuti wina aliyense angamvetsere uthenga wathu?
Yoh 10:25, 26; 15:18-20; Mac 28:23-28
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yer 7:23-26—Kudzera mwa Yeremiya, Yehova anafotokoza zokhudza anthu Ake kuti anakana mobwerezabwereza uthenga umene aneneri Ake ankawauza
Mt 13:10-16—Yesu anafotokoza kuti mofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya Yesaya, anthu ambiri adzamva uthenga wabwino koma adzakana kutsatira zimene amvazo
N’chifukwa chiyani sitimadabwa anthu ambiri akamanena kuti ndi otanganidwa moti sakufuna kumvetsera uthenga wathu?
N’chifukwa chiyani anthu ena amamvetsera ulendo woyamba koma kenako n’kusiya kuphunzira?
Ndi zitsanzo ziti zimene zingatithandize ngati anthu akutsutsa uthenga umene tikulalikira?
Kodi timatani anthu ena akamafuna kutiletsa kulalikira?
N’chiyani chimatitsimikizira kuti anthu ena akhoza kumvetsera uthenga wabwino?
Kodi anthu amene amalalikira uthenga wabwino adzayankha chiyani kwa Mulungu?
Mac 20:26, 27; 1Ak 9:16, 17; 1Ti 4:16
Onaninso Eze 33:8
N’chifukwa chiyani tifunika kulalikira kwa anthu amitundu yonse kuphatikizapo azipembedzo zonse komanso mayiko onse?
Mt 24:14; Mac 10:34, 35; Chv 14:6
Onaninso Sl 49:1, 2