Kuganiza bwino
N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kumaganiza bwino?
Onaninso 1Ti 3:2, 3
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 18:23-33—Yehova anachita zinthu moleza mtima polola Abulahamu kufunsa mafunso okhudza kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora
Ge 19:16-22, 30—Yehova anamuganizira Loti polola zimene anapempha kuti athawire ku Zowari m’malo mothawira kumapiri
Yesu anasonyeza kuganiza bwino pochita zimene mayi wa ku Foinike anapempha chifukwa chakuti anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chachikulu