Kusakhala Pabanja
N’chifukwa chiyani kusakhala pabanja kukhoza kukhala kwabwino?
N’chifukwa chiyani n’kulakwa kukakamiza m’bale kapena mlongo kuti akwatire kapena kukwatiwa?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Aro 14:10-12—Mtumwi Paulo anafotokoza chifukwa chake n’kulakwa kuweruza Akhristu anzathu
1Ak 9:3-5—Mtumwi Paulo anali ndi ufulu wokwatira; komabe, chifukwa choti sanali pabanja, ankatha kuchita zambiri potumikira Yehova
Kodi anthu omwe sali pabanja ayenera akuganiza kuti akufunika kukhala pabanja n’cholinga choti azikhala moyo wosangalala?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Owe 11:30-40—Mwana wamkazi wa Yefita anasankha kusakhala pabanja koma ankakhala moyo wosangalala potumikira panyumba ya Yehova
Mac 20:35—Ngakhale kuti Yesu sanakwatire, mawu akewa akusonyeza kuti ankakhala mosangalala chifukwa cha zimene ankachita pothandiza ena
1At 1:2-9; 2:12—Mtumwi Paulo yemwe anali wosakwatira anafotokoza mmene kuchita utumiki kunamuthandizira kukhala wosangalala chifukwa choti anathandiza anthu ambiri kudziwa Yehova
N’chifukwa chiyani anthu omwe sali pabanja mofanana ndi atumiki a Yehova onse, afunika kukhalabe ndi makhalidwe oyera?
1Ak 6:18; Aga 5:19-21; Aef 5:3, 4
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Miy 7:7-23—Mfumu Solomo anafotokoza mavuto amene mnyamata wina anakumana nawo chifukwa cholola kusocheretsedwa ndi mkazi wachiwerewere
Nym 4:12; 8:8-10—Msulami anayamikiridwa chifukwa cha khalidwe lake loyera
Kodi ndi malangizo ati anzeru amene angathandize munthu amene sali pabanja kusankha kukwatira kapena kukwatiwa?
Onaninso 1At 4:4, 5